24 JANUARY, 2022
RUSSIA
Alongo Awiri Omwe Ali ndi Mavuto a M’thupi Anakhalabe Olimba Atasungidwa ndi Apolisi kwa Miyezi 6
Khoti la mumzinda wa Smolensk m’boma la Leninskiy, posachedwa lipereka chigamulo pa mlandu wa mlongo Tatyana Galkevich ndi Valentina Vladimirova. Loya wa boma sananene chilango chomwe akufuna kuti anthuwa apatsidwe.
Nthawi Komanso Zimene Zinachitika
14 May, 2019
Apolisi anayamba kufufuza mlandu wa mlongo Tatyana Galkevich ndi Valentina Vladimirova. Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba za alongo awiriwa ndipo anawatsekera n’kuyamba kuwapanikiza ndi mafunso kwa maola opitirira 48. Ngakhale kuti alongowa ali ndi mavuto a m’thupi, khoti linalamula kuti akawatsekere m’ndende podikira kuzengedwa kwa mlandu wawo
22 November, 2019
Pambuyo pa miyezi yoposa 6, a Galkevich ndi a Vladimirova, anawatulutsa m’ndende ndipo anauzidwa kuti akhale pa ukaidi wosachoka pakhomo
31 December, 2019
A Vladimirova anawatengera kuchipatala atadwala kwambiri
6 August, 2020
Pambuyo pa miyezi 8, a Galkevich anawamasula pa ukaidi wosachoka pakhomo koma anauzidwa kuti asatuluke m’tawuni yakwawo. Pomwe a Vladimirova adakali pa ukaidi wosachoka pakhomo ndipo amangowalola kuti azilankhulana ndi wachibale wawo mmodzi yekha komanso loya
2 October, 2020
Apolisi ananena kuti a Galkevich ndi a Vladimirova ndi olakwa ndipo mlandu wawo anaulemba pachikalata chamapepala 400. M’chikalatacho analemba kuti alongowa anali ndi mlandu “wobisa zinsinsi za gulu lochita zinthu zoopsa”
14 October, 2020
Pa nthawi yomvetsera mlanduwu kwa nthawi yoyamba, jaji analamula kuti mlanduwu ubwererenso kwa loya wa boma kuti akaufufuzenso bwinobwino chifukwa umboni wake unali wosakwanira kuti ugwiritsidwe ntchito m’khoti. Ngakhale kuti a Vladimirova sanakwanitse kukapezeka kukhoti pa nthawi ya mlandu wawo chifukwa choti ankadwala, khoti linakana kuwamasula pa ukaidi wosachoka pakhomo
25 February, 2021
Khoti la apilo linakana kuti mlandu ubwererenso kwa loya wa boma, ndipo anati mlanduwu uyenera kupitirira
Zokhudza Alongowa
Ndi pemphero lathu kuti Yehova apitirize ‘kupereka mphamvu ndi kuteteza’ mlongo Galkevich ndi Vladimirova komanso abale ndi alongo athu onse omwe akuzunzidwa ku Russia ndi ku Crimea.—Salimo 28:7.