Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pamwamba (kulowera kumanzere): M’bale Aleksey Arkhipov ndi mkazi wake Natalya; M’bale Dmitriy Mikhaylov ndi mkazi wake Yelena

M’munsi (kulowera kumanja) Mlongo Svetlana Ryzhkova ndi Mlongo Svetlana Shishina

22 JULY, 2022
RUSSIA

Amboni a ku Shuya Akupirira Zinthu Zopanda Chilungamo

Amboni a ku Shuya Akupirira Zinthu Zopanda Chilungamo

Posachedwa khoti la Mzinda wa Shuya m’Chigawo cha Ivanovo lipereka chigamulo pa mlandu wokhudza M’bale Aleksey Arkhipov, Dmitriy Mikhaylov ndi mkazi wake Yelena komanso wokhudza Mlongo Svetlana Ryzhkova ndi Mlongo Svetlana Shishina. Loya waboma sananene kuti anthuwa apatsidwe chilango chotani.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 21 September, 2017

    Jaji anavomereza kuti apolisi akafufuze ndi kumvetsera zomwe M’bale Mikhaylov ankalankhulana ndi anthu pa mafoni ake

  2. 15 January, 2018

    Jaji anavomereza kuti apolisi akafufuze ndi kumvetsera zomwe Mlongo Svetlana Ryzhkova ankalankhula ndi anthu pa foni yake. Komanso kuti akaone mavidiyo omwe kamela yapanyumba pa mlongoyu inajambula

  3. 20 April, 2018

    Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba za Amboni onse okwana 5

  4. 29 May, 2018

    Apolisi anamanga M’bale Mikhaylov ndipo anamutsegulira mlandu wothandiza komanso kuyendetsa gulu lochita zinthu zoopsa. Kenako anamutsekera m’ndende poyembekezera kumuzenga mlandu

  5. 22 June, 2018

    M’bale Arkhipov anamuphatikizanso pa mlanduwu ndipo analamulidwa kuti asatuluke m’dera lomwe amakhala

  6. 27 June, 2018

    Mlongo Yelena Mikhaylova, Svetlana Ryzhkova ndi Mlongo Svetlana Shishina anawaphatikizanso pa mlanduwu

  7. 15 November, 2018

    Khoti la apilo linalamula kuti M’bale Mikhaylov amutulutse m’ndende momwe anakhalamo pafupifupi miyezi 6

  8. 10 August, 2021

    Mlandu unayamba kuzengedwa

  9. 16 September, 2021

    Mlandu unabwezedwa kwa loya waboma kuti akauwonenso bwinobwino

  10. 25 May, 2022

    Mlandu unayambiranso kuzengedwa

Zokhudza Anthuwa

Timasangalala kwambiri tikaganizira kulimba mtima komanso kupirira komwe abale ndi alongo athu ku Russia akusonyeza.—1 Atesalonika 2:20.