Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kumanzere kupita kumanja: M’bale Yevgeniy Grinenko, Sergey Kobelev ndi Mlongo Svetlana Yefremova

19 MAY, 2022
RUSSIA

Anakhala Okhulupirika Pamene Ankayesedwa ku Lesozavodsk

Anakhala Okhulupirika Pamene Ankayesedwa ku Lesozavodsk

Posachedwa Khoti la m’Boma la Lesozavodskiy m’Chigawo cha Primorye lipereka chigamulo pa mlandu okhuza M’bale Yevgeniy Grinenko, Sergey Kobelev ndi M’longo Svetlana Yefremova. Loya wa boma sananene chilango chomwe akufuna kuti anthuwa apatsidwe.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 12 May, 2020

    A Grinenko anawatsegulira mlandu wotsogolera ntchito za “gulu lochita zinthu zoopsa”. Apolisi a FSB anakafufuza zinthu m’nyumba ya a Grinenko komanso a Kobelev. Apolisi ena anapita kuntchito kwa a Kobelev komwe anakawamanga. Anawafunsa mafunso kwa maola 4 kenako anawasiya. A Grinenko nawonso anamangidwa ndipo anawaika m’ndende mongoyembekezera

  2. 14 May, 2020

    Khoti linalamula kuti a Grinenko aikidwe m’ndende mongoyembekezera

  3. 29 May, 2020

    Apolisi anasamutsa a Grinenko m’ndende yomwe anali n’kupita nawo ku ndende ya ku Spassk-Dalny

  4. 8 July, 2020

    Khoti linatulutsa a Grinenko m’ndende ndi kuwaika pa ukaidi osachoka panyumba

  5. 6 February, 2021

    A Grinenko anawamasula pa ukaidi osachoka panyumba koma anawalamula kuti asatuluke m’dera lawo

  6. 8 March, 2021

    Apolisi anatsegulira mlandu a Kobelev chifukwa chogwira ntchito ndi “gulu lochita zinthu zoopsa”

  7. 6 April, 2021

    Mlongo Yefremova anakhudzidwanso ndi mlanduwu

Zokhudza Anthuwa

Abale ndi alongo athu okhulupirika akusonyeza chitsanzo chabwino kwambiri chokhalabe olimba mtima pokumana ndi ‘masautso ambiri kuti akalowe mu ufumu wa Mulungu.’—Machitidwe 14:22.