30 AUGUST, 2022
RUSSIA
‘Anapitirizabe Kudalira Yehova’
Posachedwa khoti la Mzinda wa Bikinskiy m’Chigawo cha Khabarovsk lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Sergey Kazakov. Loya waboma sananene chilango chimene akufuna kuti khoti lipereke kwa m’baleyu.
Nthawi Komanso Zimene Zinachitika
9 November, 2020
Mlandu unatsegulidwa. M’bale Kazakov anazengedwa mlandu wotsogolera gulu lochita zinthu zoopsa
21 December, 2020
Komiti yofufuza mlandu komanso apolisi a FSB anakafufuza zinthu m’nyumba zokwana 10 kuphatikizapo ya a Kazakov. Kenako apolisi anamanga a Kazakov n’kukawatsekera poyembekezera kuwazenga mlandu
23 December, 2020
Anawatsekera m’ndende podikirira kuwazenga mlandu
4 June, 2021
Anawatulutsa m’ndende ndi kuwaika pa ukaidi wosachoka panyumba
5 August, 2021
Anawamasula pa ukaidi wosachoka panyumba
28 February, 2022
Mlandu unayamba kuzengedwa. Panthawi yomvetsera mlandu, jaji anabwezanso mlanduwu kwa loya waboma chifukwa cholephera kutsatira ndondomeko yoyenera.
28 April, 2022
Jaji anasintha zomwe ananena kuti mlandu ubwerere kwa loya waboma ndipo analamula kuti khoti lomwe linayamba kuzenga mlanduwu liyambirenso
14 June, 2022
Mlandu unayambiranso kuzengedwa
Zokhudza M’baleyu
Pamene M’bale Kazakov akupitirizabe kudalira Yehova, ifenso tikugwirizana naye kuti mawu opezeka pa Salimo 31:14 ndi oona. Mawuwa amati: “Ine chikhulupiriro changa chili mwa inu Yehova. Ndipo ndikunena kuti: ‘Inu ndinu Mulungu wanga.’”