Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kumanzere: M’bale Yuriy Baranov ndi mkazi wake, Nadezhda. Kumanja: M’bale Nikolay Stepanov ndi mkazi wake, Alla

8 JUNE, 2022
RUSSIA

Ankathandizidwa ndi Akhristu Anzawo

Ankathandizidwa ndi Akhristu Anzawo

Pa 5 September 2022, khoti la mzinda wa Volgoda linagamula kuti M’bale Yuriy Baranov komanso M’bale Nikolay Stepanov ndi olakwa. Khotili linalamula kuti M’bale Baranov azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo kwa zaka 4. Panopa m’baleyu sakuyenera kukakhala kundende. M’bale Stepanov analamulidwa kuti azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo kwa zaka 4. Chigamulochi chinayamba kugwira ntchito nthawi yomweyo.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 19 December, 2019

    Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba za mabanja 6 a Mboni za Yehova ku Vologda. A Baranov ndi a Stepanov anamangidwa ndipo anawatsekera m’ndende yongoyembekezera

  2. 20 December, 2019

    A Baranov anawatulutsa m’ndende ndi kuwaika pa ukaidi wosachoka panyumba

  3. 23 December, 2019

    A Stepanov anawapititsa kundende poyembekezera kuwazenga mlandu

  4. 16 March, 2020

    A Baranov anawamasula pa ukaidi wosachoka panyumba koma anawaletsa kulankhulana ndi aliyense wokhudzidwa ndi mlanduwu komanso anawaletsa kugwiritsa ntchito foni ndi intaneti

  5. 19 May, 2020

    A Baranov anawachotsera ziletso

  6. 13 August, 2020

    A Stepanov anawatulutsa kundende ndi kuwaika pa ukaidi wosachoka panyumba

  7. 25 September, 2020

    A Stepanov anawamasula pa ukaidi wosachoka panyumba

  8. 7 March, 2022

    Mlandu unayamba kuweruzidwa

Zokhudza Abalewa

Ndi zolimbitsa chikhulupiriro kuona abale athu akupitirizabe kukhala okhulupirika ngakhale kuti akuzunzidwa​—1 Atesalonika 3:7