Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’mwamba (kuyambira kumanzere): M’bale Vyacheslav Ivanov ndi Aleksandr Kozlitin

Mmunsi (kuyambira kumanzere): M’bale Sergey Kulakov, Mlongo Tatyana Kulakova, ndi M’bale Yevgeniy Yelin

2 NOVEMBER 2021
RUSSIA

Anthu 5 Amene Akuimbidwa Mlandu ku Sakhalin Akudalira Yehova

Anthu 5 Amene Akuimbidwa Mlandu ku Sakhalin Akudalira Yehova

Nthawi ndi Zochitika

  1. Khoti la mu Mzinda wa Nevelskiy M’chigawo cha Sakhalin, posachedwapa lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Vyacheslav Ivanov, M’bale Aleksandr Kozlitin, M’bale Sergey Kulakov, Mlongo Tatyana Kulakova, ndi M’bale Yevgeniy Yelin. * Woimira boma pa mlanduwu, sanatchule chilango chimene akufuna kuti anthuwa apatsidwe.

  2. July 2020

    A Vyacheslav, a Aleksandr, a Sergey, ndi a Tatyana anawalamula kuti asatuluke m’dzikolo

  3. 2 April, 2020

    A Yevgeniy analamulidwa kuti asatuluke m’dzikolo

  4. 20 January, 2019

    Apolisi a gulu la FSB, omwe ndi apolisi amene amafufuza zinthu mwachinsinsi ku Russia, anakachita chipikisheni pafupifupi nyumba 11 za nzika za m’dzikolo zomwe ankaziganizira kuti ndi za Mboni za Yehova. Apolisiwo anachita zinthu mwankhanza ndipo anafunsa mafunso ana ang’onoang’ono a m’mabanjawa. Zimenezi zinachitika patangopita kanthawi kochepa kuchokera pamene a pulezidenti a ku Russia, a Vladimir Putin, analonjeza kuti achitapo kanthu pa nkhani ya kuzunzidwa kwa a Mboni za Yehova.

Zokhudza Abalewa ndi Mlongoyu

Tikudziwa kuti Yehova apitiriza kusamalira abale ndi alongo athu okondedwawa, pamene akuvomereza mawu amene mneneri Yesaya ananena akuti: “Mulungu ndiye chipulumutso changa. Ndidzamukhulupirira ndipo sindidzaopa chilichonse.”—Yesaya 12:2.

^ Tsiku lenileni lopereka chigamulo nthawi zina silimadziwikiratu.