Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Igor Avramenko, yemwe wamwalira posachedwapa, ali ndi mkazi wake Yelena

MARCH 30, 2020
RUSSIA

Apolisi a FSB ku Russia Anawononga Zinthu Pofufuza Nyumba ya M’bale Yemwe Anamwalira

Apolisi a FSB ku Russia Anawononga Zinthu Pofufuza Nyumba ya M’bale Yemwe Anamwalira

Pa 23 March, 2020, apolisi a Federal Security Services (FSB) a mumzinda wa Khabarovsk ku Russia anawononga zinthu kwambiri pomwe ankafufuza kunyumba ya M’bale Igor Avramenko, patangotha masiku 6 m’baleyu atamwalira ndi matenda a mtima. Apolisiwo anaonetsa Mlongo Avramenko chikalata chowaloleza kufufuza kunyumbayo, chomwe chinali ndi dzina la M’bale Avramenko. Apolisiwo analanda kompyuta, kamera komanso zinthu zina za mlongo Avramenko ngakhale kuti M’baleyu anali atamwalira.

Tsiku lomwelo zimenezi zisanachitike, apolisiwo anapita kuntchito kwa Mlongo Avramenko kukamutenga kuti apite naye kunyumba kwake. Atafika kunyumbako n’kumene anapeza wapolisi yemwe amatsogolera ofufuzawo, dzina lake Stanislav Grebenkin akuwadikilira ndi chikalata chowalola kufufuza. Mlongoyu anauza a Grebenkin kuti mwamuna wawo anamwalira. Ngakhale kuti ankadziwa zimenezi, a Grebenkin anapitirizabe kufufuza ponena kuti anapatsidwa mphamvu zodzafufuza kunyumbayo zisanadziwike kuti M’bale Avramenko anali atamwalira.

Apolisiwo anauza Mlongo Avramenko kuti angofufuza m’nyumbayo mwamwambo chabe n’cholinga choti “atseke mlanduwo mwamsanga n’kutumiza lipoti la mlanduwo ku ofesi ya [FSB].” Komabe iwo anayamba kufufuza komanso kuwononga zinthu kwambiri.

A Mboni za Yehova okwana 10 anawatsegulira mlandu mumzinda wa Khabarovsk. Ngakhale kuti aboma akuyesetsa kuti afooketse chikhulupiriro cha abale ndi alongo athu ku Russia, tikudziwa kuti abalewa ‘akhalabe amphamvu akakhala osatekeseka ndi chikhulupiriro mwa Atate wathu wachikondi, Yehova.’​—Yesaya 30:15.