Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Apolisi ndi agulu lachitetezo la FSB akuchita chipikisheni m’nyumba za abale ku Nizhny Novgorod mu 2019

JULY 15, 2020
RUSSIA

Apolisi ku Russia Achita Chipikisheni Nyumba za Abale Zambirimbiri

Apolisi ku Russia Achita Chipikisheni Nyumba za Abale Zambirimbiri

Apolisi onyamula mfuti anakachita chipikisheni nyumba za abale zokwana 110 m’chigawo cha Voronezh, pa 13 July 2020. Izi zadziwika malinga ndi zimene chikalata china cha boma chanena. Chiyambire mu 2017, aka n’koyamba kuti apolisi achite chipikisheni nyumba za abale zambiri chonchi patsiku limodzi. Abale awiri omwe ndi Aleksandr Bokov ndi Dmitrii Katyrov, anamenyedwa komanso kuchititsidwa manyazi chifukwa chokana kupereka ma pasiwedi a mafoni awo.

Khoti la ku Leninsky m’chigawo cha Voronezh, ndi limene linalamula za chipikishenichi. Apolisiwo anakachita chipikishenichi m’mizinda yosachepera 7, m’matawuni komanso m’midzi ya m’chigawochi. Abale athu ena ambiri anatengedwa kuti akafunsidwe mafunso.

Tsiku lotsatira pa 14 July 2020, khotili linalamula kuti abale 10 atsekeredwe m’ndende podikira mlandu wawo pa 3 September 2020. Abale ake ndi awa: Aleksei Antiukhin wazaka 44, Sergey Bayev wazaka 47, Iurii Galka wazaka 44, Valeriy Gurskiy wazaka 56, Vitalii Nerush wazaka 41, Stepan Pankratov wazaka 24, Igor Popov wazaka 54, Evgenii Sokolov wazaka 44, Mikhail Veselov wazaka 51, ndi Anatoliy Yagubov wazaka 51.

Ngakhale kuti chikalatachi chinatchula za nyumba zokwana 110, panopa mabanja 100 a abale ndi alongo ndi amene avomereza kuti izi zinachitikadi m’nyumba zawo ndipo chiwerengerochi chikhoza kuwonjezeka. N’zovuta kuti tilankhulane ndi abale onse amene izi zawachitikira chifukwa choti analandidwa mafoni ndi makompyuta pa chipikishenicho.

M’mbuyomu nthawi imene chipikisheni chinachitika m’nyumba za abale ambiri, panali pa 10 February 2020, pamene apolisi anakachita chipikisheni nyumba zokwana 50 za a Mboni ku Transbaikal ku Russia. Kuchokera pamene Khoti Lalikulu Kwambiri linapereka chigamulo mu 2017, apolisi akhala akuchita chipikisheni m’nyumba zoposa 1000 za abale athu.

Malinga ndi zimene Baibulo linaneneratu, sitikudabwa ndi mayesero okhala ngati moto amene abale athu akukumana nawo ku Russia ndi m’mayiko ena. Tikupitirizabe kupempherera abale athu ndipo tikudziwa kuti Yehova awapatsa mzimu woyera kuti uwathandize kukhalabe okhulupirika.—1 Petulo 4:12-14, 19.