SEPTEMBER 7, 2020
RUSSIA
Banja Lachinyamata Litha Kupezeka Lolakwa ku Russia
Tsiku Lopereka Chigamulo
Pa 16 September 2020, * khoti la m’boma la Sverdlovskiy mumzinda wa Kostroma likuyembekezeka kulengeza chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Sergey Rayman ndi mkazi wake Valeriya. Aliyense atha kupatsidwa chigamulo chakuti azitsatira malamulo ena ali kunyumba.
Zokhudza M’bale ndi Mlongoyu
Sergey Rayman
Chaka Chobadwa: 1996 (Ku Kineshma, M’chigawo cha Ivanovo)
Mbiri yake: Anapanga maphunziro a ntchito zomangamanga pa sukulu inayake. Anakhala katswiri wokongoletsa mkati mwa nyumba. Agogo ake aakazi anamphunzitsa mfundo za m’Baibulo zomwe amazikonda ndi kuzigwiritsa ntchito pamoyo wake. Mu 2015 anakwatirana ndi Valeriya. Amakonda kuphika ndi kukaswera mu sinowo
Valeriya Rayman
Chaka chobadwa: 1993 (Ku Sharya, M’chigawo cha Kostroma)
Mbiri yake: Bambo ake anamwalira ali ndi zaka 10. Mayi ake anamuphunzitsa zokhudza Yehova. Amagwira ntchito yokonza tsitsi
Milandu Yawo
M’mawa wa pa 25 July 2018, apolisi apadera okhala ndi zida anagwiritsa ntchito zitsulo pothyola nyumba ya M’bale ndi Mlongo Rayman. Kenako apolisi anamanga banjali.Mlongo Rayman anasungidwa m’ndende masiku awiri. Pomwe M’bale Rayman anakhala m’ndende yayekha kwa masiku 59. Apolisi akhazikitsa malamulo okhwima kuti banjali lisamathe kulankhulana ndi a Mboni za Yehova anzawo. Auzanso banjali kuti lisamachoke pakhomo madzulo. Zimenezi zachititsa kuti banjali lizivutika ndi nkhawa komanso zakudza thanzi lawo.
Pamene banjali likuyembekezera kumva chigamulo chomwe khoti lingapereke, ndi pemphero lathu kuti apitirize kukhala olimba mtima komanso amphamvu, podziwa kuti Yehova sadzasiya kuwathandiza.—Yoswa 1:9.
^ ndime 3 Detili likhoza kusinthidwa