SEPTEMBER 25, 2020
RUSSIA
Banja Loyamba Kuikidwa M’ndende Poyembekezera Mlandu Wawo ku Russia Likhoza Kupezeka Lolakwa Limodzi ndi Alongo Ena Awiri
Tsiku Lopereka Chigamulo
Pa 21 October 2020, * khoti la m’boma la Pervomayskiy mumzinda wa Omsk, likuyembekezeka kupereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Sergey Polyakov, mkazi wake Anastasia, komanso Mlongo Gaukhar Bektemirova ndi Mlongo Dinara Dyusekeyeva. Loya woimira boma pa mlanduwu anapempha khoti kuti ligamule kuti M’bale Polyakov akakhale kundende zaka 6 ndi hafu. Alongo atatuwa akuyembekezeka kupatsidwa chigamulo chakuti azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo kwa zaka ziwiri.
Zokhudza M’baleyu ndi Alongowa
Sergey Polyakov
Chaka chobadwa: 1972 (M’chigawo cha Murmansk)
Mbiri yake: Anapita kukoleji ndipo anakhala katswiri wa sayansi younika mkati mwa thupi la munthu. Mu 2003, anakwatira Anastasia
Anastasia Polyakova
Chaka chobadwa: 1984 (M’chigawo cha Murmansk)
Mbiri yake: Anapita kukoleji ndipo anachita maphunziro azamalamulo. Iye ndi Sergey amakonda kuphunzira zinenero monga, Chitchainizi, Chikazaki, Chinenero Chamanja cha ku Russia ndi Chisebiya
Gaukhar Bektemirova
Chaka chobadwa: 1976 (Ku Uryl, Kazakhstan)
Mbiri yake: Ndi womaliza m’banja la ana 6. Anakulira m’dera lamapiri ku Kazakhstan ndipo amasangalala kwambiri ndi zinthu za m’chilengedwe. Kwa zaka zambiri ankafunitsitsa atadziwa cholinga chenicheni cha moyo. Kenako anapeza mayankho omveka bwino komanso okhutiritsa m’Baibulo. Kuwerenga Mawu a Mulungu mwakhama kunamuthandiza kuti apeze mphamvu komanso atonthozedwe pamene anaikidwa m’ndende ngakhale kuti sanalakwe
Dinara Dyusekeyeva
Chaka chobadwa: 1982 (Ku Leningradskove, Kazakhstan)
Mbiri yake: Ali wamng’ono ankafunitsitsa atadziwa cholinga cha moyo. Ali ndi zaka 17, anayamba kuphunzira Baibulo. Anasangalala kwambiri kudziwa nzeru zomwe zili m’Baibulo komanso dzina la mlembi wake wamkulu, Yehova. Amakonda kusewera basketball, volleyball, kuthamanga komanso kupalasa njinga
Milandu Yawo
Usiku wa pa 4 July 2018, M’bale Polyakov ndi mkazi wake Anastasia akugona, kunabwera apolisi okhala ndi zida ndipo anathyola chitseko cha nyumba yawo n’kulowa m’nyumbamo. Apolisiwo anavala zophimba kumaso ndipo anamenya kwambiri M’bale Polyakov. Kenako anamanga M’baleyu ndi mkazi wake n’kukawatsekera poyembekezera kuwazenga mlandu. Ili ndi banja loyamba kumangidwa kuchokera pamene Khoti Lalikulu Kwambiri linaletsa ntchito ya Mboni za Yehova ku Russia mu 2017. Apolisi anasiyanitsa banja la a Polyakov n’kuika aliyense m’ndende yayekha kwa miyezi 5. Kenako anawauza kuti kwa miyezi itatu akhale pa ukaidi wosachoka panyumba.
Mu May 2019, apolisi anayambiranso kuchita zipikisheni m’nyumba za Mboni za Yehova m’chigawo cha Omsk mosatsatira malamulo. Ndipo zotsatira zake n’zakuti Mlongo Bektemirova ndi Mlongo Dyusekeyeva anamangidwa. Milandu yawo inaphatikizidwa ndi ya banja la a Polyakov ndipo pa 1 April 2020, inayamba kuzengedwa.
Tikukhulupirira kuti Yehova apatsa atumiki akewa mphamvu kuti ziwathandize kupilira zinthu zopanda chilungamozi.—Aefeso 3:20.
^ ndime 3 Detili likhoza kusinthidwa