JULY 4, 2019
RUSSIA
Boma la Russia Likupitiriza Kulanda Malo a Mboni za Yehova a Ndalama Zopitirira Madola 57 Miliyoni
Kuchokera pa 20 April, 2017, pamene Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia linagamula kuti a Mboni za Yehova asamalambirenso m’dzikolo, abale ndi alongo athu akhala akuchitiridwa nkhanza zosiyanasiyana komanso kuikidwa m’ndende. Komanso malo 131 omwe panamangidwa zinthu zosiyanasiyana omwe eniake ndi a Mboni za Yehova anatengedwa ndi akuluakulu a boma. Kuonjezera pamenepo, malo okwana 60 ali pachiopsezo choti akhoza kulandidwanso. Malo onsewa ndi a ndalama zopitirira madola 57 miliyoni a ku America.
Amodzi mwa malo amene analandidwa ndi omwe panali ofesi ya nthambi ya ku Russia ku Solnechnoye. Malowa anali a bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. (Onani chithunzi chili pamwambapa kumanzere.) Malo amenewa okha ndi a ndalama zokwana pafupifupi madola 30 miliyoni. Malo enanso okwana 43 omwe analandidwa anali a mabungwe a Mboni a ku mayiko ena monga Austria, Denmark, Finland, Netherlands, Norway, Portugal, Spain, Sweden, ndi United States. Zomwe bomali linachita polanda malowa n’zosavomerezeka ndi malamulo chifukwa chigamulo cha Khoti Lalikulu Kwambiri choletsa chipembedzo cha Mboni za Yehova sichinapatse ufulu boma kuti lilande malo omwe eniake ndi a mayiko ena.
A Mboni za Yehova anakadandaula ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe (ECHR) pa nkhani ya kulandidwa kwa malo omwe panali ofesi ya nthambi ya ku Russia. Mulimonse mmene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe ligamulire nkhaniyi, ife tikudalira ndiponso kukhulupirira Yehova. Ndi pemphero lathu kuti abale ndi alongo athu ku Russia apitirize kukhala olimba mtima ndipo asalole kuti zomwe boma la Russia likuchita powathyolera nyumba, kuwamanga, kapena kuwalanda malo olambiriramo ziwalepheretse kupitiriza kulambira Yehova “motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.”—Yohane 4:23.