18 NOVEMBER, 2016
RUSSIA
GAWO 2 Nkhani Zowonjezera
Kucheza ndi Akatswiri—Akatswiri Ena Akana Kuti Boma la Russia Liletse Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Nkhaniyi ndi yachiwiri pa nkhani zitatu zomwe zikufotokoza zimene akatswiri ena ananena.
M’tsogoleri wa dziko la Russia a Vladimir Putin anakhazikitsa lamulo loti pasapezeke chilichonse choletsa kugwiritsa ntchito mawu ena a m’mabuku opatulika. Koma patangodutsa nthawi yochepa chikhazikitsireni lamuloli, akuluakulu ena a boma akufunabe kuletsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lomwe limafalitsidwa ndi Mboni za Yehova, ponena kuti lili m’gulu la zinthu zoopsa. Mlandu wa Baibuloli unaimitsidwa kaye poyembekezera kuti bungwe lina loona za maphunziro a chikhalidwe cha anthu lifufuze za Baibuloli. Podikira kufufuzaku, akatswiri ena akhala akufotokozapo maganizo awo pa nkhaniyi. Akatswiriwa ndi a zachipembedzo, zandale, zachikhalidwe cha anthu komanso a maphunziro a ulamuliro wa Soviet Union.
Kodi Akatswiri a Baibulo anenapo zotani zokhudza Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika? Nanga Anena Zotani Zokhudza Mmene a Mboni za Yehova Anamasulirira Baibuloli?
Dr. Ringo Ringvee ndi nduna yoona za m’dziko ku Estonia, mlangizi pa nkhani zachipembedzo komanso pulofesa wa zamaphunziro a chipembedzo pa sukulu ina ya zachipembedzo ku Estonia. Dr Ringvee ananena kuti: “Mofanana ndi Mabaibulo ena onse amene anamasuliridwa, omasulira Baibulo la Dziko Latsopano anayesetsa kumasulira molondola malemba a m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo. Baibulo lililonse lomwe linamasuliridwa ndi chipembedzo chinachake limasonyeza mfundo inayake yaikulu ya chipembedzocho ndipo zimenezi n’zofanananso ndi Baibulo la Dziko Latsopano. Baibuloli linagwiritsa ntchito kwambiri dzina lakuti “Yehova” komabe zimenezi sizinasinthe uthenga wa m’Baibulo. Mu 2014, anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano mu Chiesitoniya. Akatswiri azipembedzo zosiyanasiyana omwe amaona za maphunziro komanso ena omwe amamasulira Mabaibulo m’chinenerochi, anachita chidwi kwambiri ndi Baibulo la Dziko Latsopano moti ananena kuti ndi lomveka bwino komanso losangalatsa. Patangopita nthawi yochepa chitulutsireni Baibulo la Chiesitoniyali mu 2014, Baibuloli linapatsidwa mphoto ndi Unduna Woona za Kafukufuku ndi Maphunziro, m’dzikolo.”
Dr. Roman Lunkin ndi mtsogoleri pa malo ena a zamaphunziro achipembedzo ndi chikhalidwe cha anthu komanso ndi mtsogoleri wa bungwe lina la akatswiri a zachipembedzo ndi zamalamulo ku Russia. Dr Lunkin anati: “Akatswiri oona zamaphunziro achipembedzo amaona kuti a Mboni za Yehova anamasulira bwino kwambiri Baibulo lawo chifukwa analimasulira m’njira yoti mfundo zofunika kwambiri za m’Baibulo zionekere. Anthu ambiri amadziwa kuti Baibulo la Mboni za Yehova linamasuliridwa bwino kwambiri.”
Dr. Ekaterina Elbakyan ndi pulofesa woona za chikhalidwe cha anthu payunivesite ina, amagwiranso ntchito m’bungwe lina loona za maphunziro a zachipembedzo ku Europe komanso ndi mkonzi wa dikishonale ndiponso mabuku ena amaphunziro a chipembedzo ku Russia. Dr. Elbakyan anati: “Kulikonse anthu amadziwa kuti kuli Mabaibulo osiyanasiyana. Poyamba Baibulo la Chipangano chakale analimasulira m’Chigiriki n’kupanga Baibulo la Septuagint lomwe kenako analimasulira n’kupanga Mabaibulo a zinenero zosiyanasiyana kuphatikizapo Chirasha. N’zoona kuti Baibulo la chinenero chilichonse limatha kufotokozera mawu ena m’njira yosiyana ndi Baibulo la chinenero china potengera mmene chilankhulocho chilili. Komabe chofunika n’choti uthenga wa m’Baibulo loyambiriralo ukhale womwewo. Ineyo ndimaona kuti Baibulo la Dziko Latsopano analimasuliranso choncho.”
Dr. Gerhard Besier, a ku Germany ndi pulofesa wa zamaphunziro a ku Europe, ndi mphunzitsi payunivesite ya Stanford komanso ndi mkulu wa pamalo ena ochita kafukufuku wa ufulu wa anthu ndi ulamuliro wa demokalase. Dr. Besier anafotokoza kuti: “Akatswiri a Baibulo a zipembedzo zosiyanasiyana padziko lonse amayamikira kwambiri Baibulo la Dziko Latsopano.”
Dr. Liudmyla Fylypovych, ndi pulofesa komanso ndi mkulu wa dipatimenti yoona za mbiri ya zipembedzo pamalo ena amaphunziro azachipembedzo ndi zasayansi komanso ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa bungwe lina la akatswiri oona za chipembedzo ku Ukraine. Dr. Fylypovych ananena kuti: “Amene anamasulira Baibulo la Mboni za Yehova si anthu wamba koma ndi odziwa ntchito yawo omwe akhala akugwira ntchitoyi kwa zaka zambiri mothandizidwa ndi akatswiri odziwa zilankhulo zingapo ndi enanso odziwa zilankhulo zakale za Baibulo. Akatswiri osiyanasiyana makamaka a Baibulo atafufuza bwino za Baibulo la Dziko Latsopano ananena kuti Baibuloli silinasinthe uthenga wake ndipo n’chimodzimodzi ndi mmene analili Mabaibulo oyambirira. Akatswiriwa sanapezenso kuti m’Baibulo la Mboni za Yehova munalembedwa mfundo iliyonse imene ingayambitse chisokonezo. Mawu omwe ankamveka achikale komanso ovuta kumvetsa anawamasulira momveka bwino komanso mogwirizana ndi mmene anthu akulankhulira masiku ano. Matchalitchi ena achikhristu amagwiritsa ntchito Baibuloli ndipo amaliona kuti ndi lothandiza pophunzitsa Baibulo padziko lonse.
Dr. George D. Chryssides anali mtsogoleri wa maphunziro achipembedzo payunivesite ya Wolverhampton, ndipo amachita kafukufuku wa zipembedzo zamakono payunivesite ya St. John ndi ya Birmingham ku United Kingdom. Dr. Chryssides anati: “Akatswiri ena sagwirizana ndi mmene anamasulira Baibulo la Dziko Latsopano. Koma ndi mbali zochepa zimene amatsutsa ndipo ndi zimene iwowo amaona kuti sizikugwirizana ndi malemba ena. A Mboni za Yehova sanawonjezere chilichonse chomwe tingati ndi choopsa kapenanso chomwe chingayambitse chisokonezo. Mosiyana ndi zimene akuluakulu a boma la Russia akunena, a Mboni za Yehova amagwiritsa ntchito Baibulo polimbikitsa mtendere komanso kutsutsa zachiwawa.
Frank Ravitch ndi pulofesa wa zamalamulo komanso mtsogoleri woona nkhani za malamulo ndi chipembedzo payunivesite ya Michigan State ku United States. A Ravitch anati: “Sindikuona kuti Baibuloli lingakhale chinthu choopsa ndipo ndimaona kuti linamasuliridwa bwino kwambiri. Ndimalankhula Chingelezi, Chijapanizi komanso Chiheberi ndipo ndimadziwa zimene zinalakwika m’Mabaibulo ena amene anamasuliridwa. Koma Baibulo la Dziko Latsopano lilibe zolakwika zimenezo ngati mmene zilili ndi Mabaibulo ena odziwika bwino ngati Baibulo loyambirira la King James.”
Dr. Ain Riistan ndi mphunzitsi wa mabuku a Chipangano Chatsopano payunivesite ya Tartu komanso ndi pulofesa pasukulu ina yamaphunziro ndi mbiri yazipembedzo yomwenso imaphunzitsa ansembe ku Estonia. Dr. Riistan anati: “Baibulo lililonse limakhala ndi zolakwika zake ndipo pali zifukwa zambiri zimene zimachititsa zimenezi. Ndimaona kuti mu Baibulo la Dziko Latsopano, muli mawu ena omwe ineyo ndikanawamasulira mwanjira ina. Ndipo ndimaonanso zimenezi m’Mabaibulo ena onse. Sindine katswiri wa Chirasha komabe chinenerochi ndimachimva bwinobwino. Choncho sindinganene ngati Baibulo la Chirasha analimasulira bwino kapena ayi. Atatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Chiesitoniya mu 2014, anthu ambiri analiyamikira kwambiri. Moti anthu ankanena kuti Baibulolo linali lapadera kwambiri m’chakacho chifukwa linali losavuta kumva. Kaya Baibulo la Dziko Latsopano alimasulira m’chinenero chiti, uthenga wake umakhala wofanana chifukwa kulikonse padziko lapansi amagwiritsa ntchito njira zofanana polimasulira ndipo zinthu zina zingasiyane pang’ono chifukwa cha kusiyananso kwa zinenero. Sindikuganiza kuti Baibulo la Chirasha lingakhale losiyana ndi la Chiesitoniya. Choncho ndikhoza kunena motsimikiza kuti Baibuloli linamasuliridwa bwino ndipo lilibe chilichonse chomwe chingayambitse chisokonezo.”
Dr. Basilius J. Groen ndi mtsogoleri woona zachikhalidwe cha anthu komanso wa zokambirana pa nkhani zachipembedzo kumayiko a kum’mwera chakum’mawa kwa Europe mu nthambi ya bungwe la United Nations yoona za maphunziro, sayansi ndi chikhalidwe cha anthu, komanso ndi pulofesa wa maphunziro a zachipembedzo ndiponso mtsogoleri wa nkhani zachipembedzo payunivesite ya Graz ku Austria. Dr. Groen anati: “N’zomvetsa chisoni kuti akuluakulu a boma amene akufuna kulanda Mabaibulo a Mboni za Yehova sadziwa chilichonse chokhudza nkhani zachipembedzo komanso Malemba Opatulika. Ngakhale kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika linamasuliridwa bwino, pali anthu ena amene sagwirizana ndi mawu ena omwe anagwiritsa ntchito polimasulira. Koma ndimaona kuti ndi mmene zilili ndi Mabaibulo ena onse ndipo ndi mmene zililinso ndi Baibulo la tchalitchi chathu cha Katolika.”
Dr. Hocine Sadok ndi mphunzitsi wa zamalamulo komanso mtsogoleri wa dipatimenti yoona za chikhalidwe cha anthu komanso za malamulo a kayendetsedwe ka chuma payunivesite ya Haute Alsace ku France. Dr. Sadok anati: “Monga katswiri wa maphunziro, ineyo ndimaona kuti Baibulo la Dziko Latsopano si Baibulo loti akuluakulu a boma angakhale pansi n’kumalifufuza. Ndi buku lachipembedzo ndipo si nkhani yoti akuluakulu a boma loyendera ulamuliro wa demokalase alowererepo. N’zosamveka kunena kuti Baibuloli lingakhale ndi uthenga womwe ungayambitse chisokonezo.
Dr. William Cavanaugh ndi pulofesa wa maphunziro a Chikatolika komanso ndi mtsogoleri woona za maphunziro Achikatolika ndi nkhani zachipembedzo padziko lonse payunivesite ya DePaul ku United States. Dr. Cavanaugh anati: “Ndimaona kuti akatswiri ambiri amaona kuti Baibulo limene a Mboni za Yehova anamasulira ndi lofunika kwambiri, ngakhale kuti pali ena amene sagwirizana ndi mmene anamasulirira mawu ndi ziganizo zina.”
Kodi munganenepo zotani pa maganizo a akuluakulu a boma la Russia ofuna kuletsa Baibulo la Mboni za Yehova ponena kuti lili ndi mfundo zoopsa?
Dr. Elbakyan a ku Russia ananena kuti: “Ndikuona kuti kuletsa kuti Baibuloli lisalowenso m’dziko la Russia n’kosemphana ndi lamulo la boma lokhudza zinthu zoopsa pa Gawo 3, lomwe a Putin omwe ndi mtsogoleri wa dzikoli anasainira m’chaka cha 2015. Lamulo limene mtsogoleriyu anasainira silinena chilichonse chokhudza ntchito yomasulira malemba opatulika. Tonse tikudziwa kuti poyamba kaya ndi Baibulo, Korani, Torah komanso Kangyur silinalembedwe m’Chirasha kapena m’Chisilavo. Mabukuwa anachita kumasuliridwa ndipo alipo ambirimbiri. Malamulo a boma la Russia sanena kuti ndi mabuku ati opatulika amene ayenera kumagwiritsidwa ntchito komanso kuti ndi ati amene ndi oletsedwa. Choncho anthu akhoza kugwiritsa ntchito buku lililonse lopatulika ndipo kuletsa buku lililonse la mabuku amenewa kungakhale kuphwanya malamulo.”
Dr. Derek H. Davis ndi loya komanso anali mtsogoleri wakale wa bungwe lina loona za maphunziro a matchalitchi ndi ulamuliro ku yunivesite ya Baylor ku United States. Dr. Davis ananena kuti: “N’zovuta kumvetsa kuti munthu angaganize zoletsa buku lililonse lodziwika kuti ndi lachipembedzo. Makamaka kuletsa Baibulo la chipembedzo chodziwika bwino cha Mboni za Yehova. Kuchokera kalekale timadziwa kuti Baibulo lawoli ndi buku lopatulika. Pali mabaibulo ambirimbiri amene amagwiritsidwa ntchito ndi zipembedzo zina zachikhristu omwe sanaletsedwe. Zikungoonekeratu kuti boma la Russia likufuna kulimbana ndi a Mboni za Yehova osati Baibulo lawoli.”
Dr. Jeffrey Haynes ndi pulofesa pa nkhani zandale komanso mkulu wa bungwe loona zamaphunziro achipembedzo komanso olimbikitsa mgwirizano pakakhala kusemphana maganizo, payunivesite ya London Metropolitan, komanso ndi tcheyamani wa gulu lina lochita kafukufuku pa nkhani za ndale ndi chipembedzo ku United Kingdom. Dr. Haynes ananena kuti: “Dziko la Russia linasainira nawo Pangano la Padziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale.” Ndiye zomwe dzikoli likuchita pofuna kuletsa Baibuloli, zikuphwanya ufulu wachipembedzo womwe mayiko anagwirizana m’panganoli.
Dr. Lunkin, a ku Russia ananena kuti: “Ku Russia, anthu amaona kuti mfundo zachipembedzo ndi zofunika kwambiri pa chikhalidwe chawo koma akuluakulu a boma ayamba kuona kuti chipembedzo n’chokayikitsa. Kodi ngati munthu wina angaganize zoletsa kugwiritsa ntchito mawu ena a m’buku lopatulika si ndiye kuti mabuku ena onse opatulikawa aletsedwanso? Panopo a matchalitchi komanso makhoti ayamba kale kusankhira anthu mabuku omwe iwowo akuwaona kuti ndi opatulika. Anthu oyamba kuvutika ndi mfundozi ndi a Mboni za Yehova chifukwa cha Baibulo lawo ndipo sizodabwitsa chifukwa andale anayamba kulimbana ndi a Mboni kuyambira mu 2009.
A William S. B. Bowring ndi pulofesa wa zamalamulo komanso mkulu woona za ufulu wa anthu payunivesite ina mumzinda wa London ku United Kingdom. A Bowring anati: “Ndikudziwa kuti boma la Russia likufuna kuletsa Baibulo la Dziko Latsopano chifukwa chakuti ndi la Mboni za Yehova. Ndipo kuchita zimenezi n’kupanda nzeru chifukwa Baibulo ndi Baibulo basi komanso Korani imakhala Korani basi ndipo zilibe kanthu kuti wamasulira ndi ndani. Sindikukayikira kuti Baibuloli analimasulira mosamala kwambiri.
Dr. William Schmidt ndi mkonzi wamkulu wa buku lina la chipembedzo komanso pulofesa woona za mgwirizano wa mayiko pamalo ena oona zamaphunziro aulamuliro komanso zachuma ku Russia. Dr. Schmidt anati: “Sindikuganiza kuti mfundo zatsopanozi anangozikhazikitsa popanda cholinga chofuna kulimbana ndi a Mboni za Yehova kapena zipembedzo zina zing’onozing’ono. Kwenikweni nkhani ndi yoti m’dzikoli muli mavuto pa nkhani zandale komanso zamalamulo chifukwa sakusiyanitsa nkhani zachipembedzo ndi zandale komanso mmene nkhanizi zimakhudzira moyo wa anthu. Mpaka pano boma la Russia lilibe mfundo komanso ndondomeko zomveka bwino zosonyeza nkhani zachipembedzo zomwe lingafunike kulowererapo. Kusamveka bwino kwa mfundo zomwe bomali likuyendera kukuchititsa kuti lizikhazikitsa mfundo zongofuna kulimbana ndi bungwe kapena gulu linalake la anthu. Zimenezi zikusokoneza mmene zipembedzozo zimafunikira kugwirira ntchito yawo komanso zikuchititsa kuti magulu komanso anthu azipembedzo zosiyanasiyana azilephera kukambirana mfundo zawo. Mfundozi zikuchititsanso kuti akuluakulu a bomali azingokayikira chilichonse chomwe azipembedzo akuchita. Chipembedzo chilichonse chimaona kuti mawu a m’mabuku opatulika ndi ofunika kwambiri ndipo chimagwiritsa ntchito mawuwo pokhazikitsa mfundo zoti anthu ake aziyendera.”
Dr. Chryssides, a ku United Kingdom ananena kuti: “Sindikuganiza kuti pali chifukwa chilichonse chomveka choti boma la Russia liletsere Baibulo la Dziko Latsopano.” M’Baibulo la a Mbonili mulibe chilichonse chomwe chingayambitse chisokonezo. Baibuloli analimasulira kuchokera ku malemba oyambirira a Chiheberi ndi Chigiriki ndipo uthenga wake ndi wofanana ndi wa m’Mabaibulo ena onse.
Dr. Thomas Bremer anali m’modzi wa anthu ochita kafukufuku wa maphunziro apamwamba okhudza dziko la Russia payunivesite ya New York, ndi pulofesa wolimbikitsa mgwirizano wa zipembedzo zachikhristu komanso woona zamaphunziro a matchalitchi a ku mayiko a kum’mawa ndi kulimbikitsa mtendere, payunivesite ya Münster ku Germany. Dr. Bremer anati: “Zikuoneka kuti kungochokera pamene akuluakulu a boma la Russia anayamba kuona chipembedzo cha Mboni za Yehova ngati gulu loopsa, anayamba kuchita zinthu zosiyanasiyana kuti azilimbana nacho. Koma palibe aliyense amene amagwirizana ndi maganizo awowa.”
Dr. Jim Beckford a ku United Kingdom anaphunzitsapo pa British Academy; anali pulofesa woona za chikhalidwe cha anthu payunivesite ya Warwick; anakhalapo mtsogoleri wa bungwe lina la maphunziro asayansi ya zachipembedzo. Dr. Beckford ananena kuti: “Sindikudabwa ndi zimene akuluakuluwa akuchita. Zikuoneka kuti akutsatira mfundo zimene ulamuliro wa Soviet Union unkachita chifukwa nawonso unkachita zomwezi polimbana ndi zipembedzo zing’onozing’ono. Koma m’malo moletsa zipembedzo zambiri, boma la Russia likupondereza zipembedzo zing’onozing’ono pobisalira pamfundo yoti likufuna kulimbana ndi zinthu zimene zingayambitse chisokonezo chachikulu.”
Dr. Dmitry Uzlaner a ku Russia. Anali mmodzi wa anthu ochita kafukufuku wa maphunziro a chikhalidwe cha anthu komanso kayendetsedwe ka zachuma payunivesite ya Moscow; ndi mkonzi wamkulu wa buku lonena za boma komanso zipembedzo. Dr. Uzlaner anati: “Chomwe chapangitsa kuti boma la Russia lilembenso zipembedzo m’kaundula wake n’chakuti: Pali zipembedzo zimene amati n’zovomerezeka ndi boma (choyamba ndi cha Russian Orthodoxy komanso pali Chisilamu, Chiyuda ndi Chibuda) ndi zina zomwe amati n’zosavomerezeka ndi boma komanso zobwera (mwachitsanzo chipembedzo cha Mboni za Yehova). Choncho potengera mfundo imeneyi, zipembedzo zomwe n’zovomereka zimayenera kupatsidwa ufulu ndi boma, pomwe zipembedzo zosavomerezeka siziyenera kupatsidwa ufulu wonse chifukwa zimaphunzitsa mfundo zachilendo kwa anthu a m’dziko la Russia. N’chifukwa chake zingakhale zovuta kuti a Mboni za Yehova komanso a zipembedzo zina zing’onozing’ono asangalale ndi lamulo latsopano lomwe likuoneka ngati cholinga chake n’chofuna kupatsa anthu ufulu wopembedza komanso kuti pasakhale lamulo loletsa mabuku 4 opatulika. Komabe ineyo ndikuona kuti Mboni za Yehova komanso zipembedzo zina zonse zing’onozing’ono za ku Russia zikuyenera kupatsidwa ufulu wopembedza womwe uli m’malamulo a dzikoli.
A Eric Rassbach ndi wachiwiri kwa loya wamkulu wa bungwe lina loona za ufulu wa zipembedzo ku United States. Iwo anati: “A Mboni za Yehova akuyenera kupatsidwa ufulu wogwiritsa ntchito Baibulo lawo. Ngati munthu wapatsidwa ufulu wopembedza sangaletsedwe kugwiritsa ntchito Malemba Opatulika ndipo pali zipembedzo zambiri zimene zimagwiritsa ntchito Mabaibulo awo. Choncho kungoletsa Baibulo la Mboni za Yehova lokha komanso kuliona ngati chinthu choopsa n’kulakwa kwakukulu komanso nkhanza chifukwa nawonso ali ndi ufulu wotsatira zomwe amakhulupirira.”
Dr. Emily B. Baran ndi wachiwiri kwa pulofesa woona za mbiri ya dziko la Russia ndi mayiko a kum’mawa kwa Europe payunivesite ya Middle Tennessee State ku United States. Iwo ananena kuti: “Kuika lamulo lililonse loletsa kugwiritsa ntchito Baibulo linalake, n’kulakwira nkhani ya ufulu wachipembedzo. Makamaka ngati lamulolo likulimbana ndi gulu linalake lachipembedzo komanso mmene gululo limafotokozera malemba. Si udindo wa boma kulowerera nkhani zachipembedzo, kaya kuonanso ngati Baibulo linalake linamasuliridwa bwino kapena ayi.”
Sir Andrew Wood a ku United Kingdom amagwira ntchito ku bungwe loona za ubale wa dziko la Russia ndi mayiko a ku Europe ndi Asia; anagwiraponso ntchito ngati kazembe wa dziko la Britain ku Russia (1995-2000). Iwo ananena kuti: “Panopa pali mgwirizano waukulu pakati pa boma la Russia ndi tchalitchi cha Russian Orthodox. Tchalitchichi ndi chosiyana kwambiri ndi matchalitchi a Orthodox a m’mayiko ena ndipo zochita zake zikufanana kwambiri ndi zimene boma la Russia likuchitanso tikaliyerekeza ndi mayiko ena. Ndikuona kuti tchalitchichi sichingalole zoti Baibulo la Dziko Latsopano lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova lizionedwa ngati buku lopatulika ngati mmene zilili ndi mabuku a zipembedzo 4 zovomerezeka ndi bomali. Zikuonekanso kuti akuluakulu a bomawa akufunanso kuletsa anthu a zipembedzo zimene zili ndi mabuku opatulika kuti asamakambirane ndi anthu ena zimene amakhulupirira. Ngakhale kuti a Mboni anayamba kupezeka m’dziko la Russia kalekale kwambiri, n’zokayikitsa ngati akuluakulu a boma angasinthe maganizo awo chifukwa sanayambe lero kulimbana ndi chipembedzo cha Mboni za Yehova.”
Dr. Fylypovych, a ku Ukraine ananena kuti: “Cholinga chimene boma la Russia likuletsera Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika komanso mabuku ena, n’choti likufuna lizisankhira anthu ake zochita pa nkhani yachipembedzo. Pofuna kukwaniritsa cholinga chakechi bomali likumaletsa komanso kuvomereza mabuku opatulika amene likufuna. Tchalitchi cha Russian Orthodox sichivomereza Baibulo la Mboni za Yehova komanso mabaibulo a zipembedzo zina. Mwachitsanzo, tchalitchichi sichivomereza Baibulo la Katolika la Vulgate. Ndipo tchalitchi cha Katolika nachonso sichivomereza Baibulo lomwe linamasuliridwa ndi Martin Luther.”
Dr. Zoe Knox ndi pulofesa wophunzitsa za mbiri ya dziko la Russia payunivesite ya Leicester ku United Kingdom. Dr. Knox anati: “Kukhazikitsa lamulo lokhudza zinthu zoopsa kungawoneke ngati cholinga chake n’kuteteza Baibulo kuti lisaletsedwe kapena kuliteteza kuti lisafufuzidwe ngati lili loyenera kuligwiritsa ntchito. Komabe m’malo moteteza uthenga wa m’baibulo, lamuloli likuletsa mabaibulo ena. Sikuti Baibulo la Dziko Latsopano likuletsedwa chifukwa cha uthenga wake koma chifukwa choti eniake a Baibulolo ndi a Mboni za Yehova. Akuluakulu a boma akuona kuti zinthu zosiyanasiyana zimene a Mboni amachita zomwe zikuphatikizapo misonkhano yawo komanso zimene amakhulupirira, zikusokoneza chikhalidwe cha anthu a m’dziko la Russia. Komanso akuluakuluwa amaona kuti chipembedzochi n’cha ku America ndipo n’chosavomerezeka m’dzikolo.”
Mayi Catherine Cosman ndi mkulu wounika ndondomeko komanso malamulo (ku Europe komanso ku mayiko omwe kale anali mu ulamuliro wa Soviet Union), ali ku nthambi ya boma la United States yoona za ufulu wa zipembedzo. Mayi Cosman ananena kuti: “Zimene boma la Russia likuchita poletsa Baibulo la Mboni za Yehova, zikusonyeza kuti bomali limaona kuti Mabaibulo ena okha ndi amene ali ovomerezeka. Ndipo kuchita zimenezi, n’kuphwanya ufulu wachipembedzo wa anthu. Boma la Russia liyenera kuonanso bwino lamulo lawo la zinthu zoopsa ngati mmene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, Komiti Yoona za Malamulo ya m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya komanso Bungwe Loona za Chitetezo ndi Mgwirizano wa Mayiko a ku Ulaya linanenera.”
Dr. Cavanaugh, a ku United States ananena kuti: “Sindikugwirizana ndi mfundo yoletsa mabuku opatulika amene anamasuliridwa. Maganizo ofuna kumalamulira zimene zipembedzo zimakhulupirira akusonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa tchalitchi cha Russian Orthodox ndi boma la Russia. Ulamuliro wa Soviet Union utatha, anthu ambiri ku Russia anali ndi nkhawa chifukwa zipembedzo zosiyanasiyana zinathamangira kukopa anthu kuti alowe m’zipembedzo zawo. Chifukwa cha zimene zinachitikazi, anthu ambiri ankaonanso kuti pakufunika nthawi yokwanira kuti tchalitchi cha Russian Orthodox chikhalenso ndi mphamvu ngati mmene zinalili poyamba.”
Dr. John A. Bernbaum a ku United States ndi pulezidenti wa payunivesite ina mumzinda wa Moscow yomwe imaphunzitsa achinyamata kuti adzakhale atsogoleri. Dr. Bernbaum ananena kuti: “Ndikugwirizana ndi maganizo oti a Mboni za Yehova akhale ndi Baibulo lawolawo potengera zimene amaphunzira m’mawu a Mulungu. Akuluakulu a boma sayenera kulowererapo pa ntchito yomasulira Baibulo kapena yofalitsa mabuku ena achipembedzo. Akuluakulu a boma ayenera kudziwa kuti munthu aliyense ali ufulu wokhala m’chipembedzo chimene akufuna komanso kufotokoza momasuka zimene amakhulupirira mogwirizana ndi zimene amaphunzira ku chipembedzocho.”
A Alexander Verkhovsky ndi mkulu wa bungwe lina la ku Russia lomwe limachita kafukufuku wokhudza ufulu wodzilamulira wa anthu, ubale wa pakati pa boma ndi zipembedzo komanso wokhudza mfundo za malamulo a zinthu zoopsa. Iwo ananena kuti: “Sitikuonamo chilichonse choyambitsa chisokonezo mu Baibulo la Dziko Latsopano. Tikuona kuti kumanga a Mboni za Yehova komanso kuletsa mabuku awo, langokhala tsankho chifukwa chosiyana zipembedzo.”
Dr. Régis Dericquebourg ndi katswiri woona za chikhalidwe cha anthu komanso pulofesa woona za zipembedzo zongoyamba kumene m’bungwe lina loona za chipembedzo ku Belgium. Iwo ananena kuti: “Sikuti a Mboni akufuna kulimbana ndi boma la Russia pogwiritsa ntchito Baibulo lawoli. Ndi Baibulo basi ngati mmene Mabaibulo ena alili. Sindikuona chimene chingapangitse kuti Baibuloli likhale chinthu choopsa. Ndipo likanakhaladi loopsa, bwenzi litaletsedwa kale m’mayiko ena omwe akulimbana ndi nkhani ya zinthu zoopsa. Komatu m’mayiko amenewa Baibuloli likupezekamo.”
Dr. Mark R. Elliott ndi mkonzi komanso amene anayambitsa magazini ina yonena za Matchalitchi payunivesite ya Asbury ku Kentucky m’dziko la United States. Dr. Elliott ananena kuti: “N’zomvetsa chisoni kuti panopo boma la Russia likumanyalanyaza ufulu wa anthu a mitundu ina komanso wa zipembedzo zing’onozing’ono. Tikatengera maganizo a tsankho omwe akuluakulu a bomawa akuchita pogwiritsa ntchito lamulo la zinthu zoopsa, ndiye kuti Baibulo lililonse likhoza kukhalanso loopsa kuphatikizapo Baibulo lawo la Russian Orthodox.”
Dr. Besier a ku Germany ananena kuti: “Zikuoneka kuti akuluakulu a boma la Russia angakonde kuti m’dzikoli mukhale Akhristu a tchalitchi cha Russian Orthodox okha komanso mabuku a tchalitchichi basi. Si a Mboni okha amene akukumana ndi mavuto ku Russia, anthu a zipembedzo zina akukumananso ndi mavutowa. Ndipo zikufanana ndi mmene zinalilinso mu ulamuliro wa Soviet Union. Boma la Russia likudana ndi chipembedzo chilichonse chomwe ndi chodziwika kwambiri ku United States.”
Dr. Silvio Ferrari. ali m’gulu lina loona za malamulo ndi maphunziro a zachipembedzo, mkonzi wamkulu wa magazini ina yonena za malamulo ndi chipembedzo, amene anayambitsa nawo bungwe lochita kafukufuku wa matchalitchi ndi maboma, pulofesa woona za malamulo komanso zachipembedzo payunivesite ya Milan ku Italy. Dr. Ferrari ananena kuti: “Nkhani yofuna kukhazikitsa lamulo lofuna kuletsa Baibulo la Mboni za Yehova la m’Chirasha ponena kuti lili m’gulu la zinthu zoopsa, ndi yachilendo ku Europe kuno. Komanso ngakhale kuti kukhazikitsa lamulo lokana kuletsa Baibulo, Korani, Tanaki ndi Kangyur komanso kugwiritsa ntchito mawu a m’mabukuwa kungaoneke kuti ndi kwabwino, zikuonetseratu kuti bomali likukondera malemba opatulika a m’zipembedzo zina. Zimenezi n’zosamveka chifukwa kusiyanitsa kumeneku kukuchitika popanda umboni uliwonse wotsimikizira kuti mabuku ena opatulika ndi oopsadi kuposa ena.”
Dr. Carolyn Evans ndi mmodzi wa akuluakulu a payunivesite ina yophunzitsa zamalamulo ku Australia komanso ndi mmodzi wa akonzi a buku lonena za zipembedzo ndi malamulo a m’mayiko. Dr. Evans anati: “Zimakhala zoopsa ngati boma layamba kusankhira anthu mabuku achipembedzo omwe angakhale ovomerezeka. Umenewu si udindo wa boma, ndi nkhani zimene anthu azipembedzo amayenera kukambirana okha. Pali Mabaibulo ndi mabuku opatulika osiyanasiyana komanso omasuliridwa mosiyanasiyana. Ndiye ngati boma lingalowerere pa nkhaniyi n’kusankhira anthu buku lopatulika loti azigwiritsa ntchito, kungakhale kuphwanya mfundo yokhudza ufulu wachipembedzo yomwe mayiko anagwirizana m’malamulo awo.”
Dr. Javier Martínez-Torrón ndi pulofesa woona zamalamulo komanso mkulu wa dipatimenti ya zamalamulo ndi chipembedzo payunivesite yophunzitsa za malamulo ku Spain. Dr. Martínez-Torrón ananena kuti: “Palibe paliponse m’malamulo a mayiko a ku Europe pomwe pamapereka mphamvu yoletsa buku lopatulika la chipembedzo chinachake pokhapokha ngati m’bukumo muli mfundo yomwe ingayambitse chidani kapena yolimbana ndi malamulo a dzikolo.”
A Robert C. Blitt ndi pulofesa wa zamalamulo payunivesite ya Tennessee; analinso katswiri wa zamalamulo ku nthambi ya boma la United States yoona za ufulu wa zipembedzo padziko lonse. Pulofesa Blitt ananena kuti: “Pangano la Mfundo za Ufulu wa Anthu Onse ndi wa Zandale, limanena kuti ‘chipembedzo ndi chovomerekezeka ndi malamulo. . . ndipo chiyenera kupatsidwa ufulu wake wonse.’ Choncho ngati boma lingapereke ufulu ku gulu linalake la chipembedzo koma n’kuikira malamulo okhwima gulu lina la chipembedzo, kungakhale kuphwanya mfundo ya mu Pangano la Mfundo za Ufulu wa Anthu Onse ndi wa Zandale yomwe imalimbikitsa kupereka chitetezo chofanana ku zipembedzo zonse komanso kuletsa kukondera zipembedzo zina chifukwa cha zimene amakhulupirira.”
Dr. Sadok a ku France ananena kuti: “Zikuoneka kuti nkhani yaikulu ndi yoti boma la Russia likulimbana ndi mayiko omwe zipembedzo zawo zili m’dzikolo osati kufuna kulimbana ndi zipembedzozo. Zimene bomali likuchita zikusonyeza kuti sakufuna kuti mayiko ena azilowererapo pa nkhani za m’dziko lawo kaya zikhale zandale kapena zachipembedzo chifukwa akuona kuti zikhoza kubweretsa chisokonezo m’dzikolo. Akuluakuluwa akuona kuti zipembedzo zing’onozing’ono ngati cha Mboni za Yehova zikupangitsa kuti mayiko ena azipezerapo mwayi wolimbana ndi ulamuliro wawo. Chifukwa cha maganizo amenewa, bomali limaona kuti a Mboni za Yehova ndi chipembedzo cha ku North America komanso ngati gulu lomwe likuchititsa kuti zinthu zisamayende bwino m’dzikolo. Choncho zoona zake n’zoti boma la Russia likulimbana ndi a Mboni mwa chiphamaso chabe.”
Dr. Marco Ventura ndi pulofesa wa zamalamulo ndi chipembedzo payunivesite ya Siena ku Italy; wamkulu wa pamalo ena a za maphunziro a chipembedzo; wochita kafukufuku pa nkhani zachipembedzo payunivesite ya Strasbourg ku France. Dr. Ventura anati: “Zomwe boma la Russia likuchita zapangitsa kuti zipembedzo komanso mabungwe azipembedzo asakhale ndi ufulu wokonza, kuitanitsa komanso kufalitsa mabuku awo momasuka. Ndipo chitsanzo chabwino ndi kuletsedwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano la Mboni za Yehova. Kuonjezera pakuletsa Baibuloli, akuluakulu a boma la Russia afika mpaka popondereza udindo wa atsogoleri azipembedzo wosankha kumasulira komanso kugwiritsa ntchito Malemba opatulika a kumtima kwawo. Akuluakuluwa akugwiritsira ntchito molakwika udindo wawo chifukwa akulowerera nkhani zosawakhudza komanso akuchita zinthu mokondera.”
Dr. Riistan, a ku Estonia ananena kuti: “Ine ndikuona kuti ndi pofunika kutsimikiza ngati m’dziko la Russia mulidi ufulu wachipembedzo. Chifukwatu si a Mboni za Yehova okha amene akuvutika m’dzikoli panopa. Ndikuonanso kuti kuletsa kuti Baibulo linalake lisamagwiritsidwe ntchito, ndi nkhani yaikulu kwambiri. Chifukwa ngati akuletsa Baibulo limodzi ndiye kuti zikutanthauza kuti Mabaibulo ena onse aletsedwanso. Ndipo ngati angaletse Mabaibulo onse, ndiye kuti ayeneranso kuletsa Baibulo loyambirira la Chiheberi, Chiaramu komanso Chigiriki. Ndiye nanga bwanji za mipukutu yoyambirira ya Baibulo, kodi sindiye kuti nayonso ikufunika kuletsedwa? Ngati sangachite zimenezi ndiye kuti pali nkhani ina yomwe bomali likufuna osati yolimbana ndi mitundu ina ya Baibulo.”
Yankhulani ndi:
International: David A. Semonian, Office of Public Information, 1-718-560-5000
Russia: Yaroslav Sivulskiy, 7-812-702-2691