Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Vladimir Alushkin asanamangidwe n’kuikidwa m’ndende

NOVEMBER 13, 2019
RUSSIA

Bungwe la UN Lapempha Boma la Russia Kuti Litulutse M’ndende M’bale Alushkin

Bungwe la UN Lapempha Boma la Russia Kuti Litulutse M’ndende M’bale Alushkin

Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka latulutsa lipoti la masamba 12 lodzudzula boma la Russia chifukwa chomanga komanso kutsekera m’ndende M’bale Vladimir Alushkin. Mu lipotili, gululi lapempha boma la Russia kuti litulutse m’ndende komanso lipereke ndalama za chipepeso choyenerera kwa m’baleyu chifukwa chomuphwanyira ufulu wake.

M’bale Alushkin anamangidwa pa 15 July, 2018, pamene apolisi pafupifupi 12 ovala zobisa nkhope omwe ananyamula mfuti analowa m’nyumba yake. Apolisiwo anapanga chipikisheni m’nyumbayo kwa maola pafupifupi 4 ndipo analanda mafoni a m’manja, zipangizo zina, Mabaibulo, komanso mabuku ena. Kenako m’baleyu anamutengera ku dipatimenti yofufuza kuti akamufunse mafunso.

M’bale Vladimir Alushkin ali kukhoti la m’boma la Pervomayskiy mumzinda wa Penza mu January 2019

Apolisi anasunga M’bale Alushkin m’ndende yongoyembekezera kwa masiku awiri. Apa n’kuti khoti la m’boma la Pervomayskiy mumzinda wa Penza lisanagamule kuti asungidwe m’ndende kwa miyezi iwiri poyembekezera kuzenga mlandu wake. Kenako khotili linaonjezera kawiri nthawi yomwe M’bale Alushkin anayenera kusungidwa m’ndende. M’baleyu anakhala m’ndende kwa miyezi pafupifupi 6 kenako anauzidwa kuti akakhale pa ukaidi wosachoka panyumba ndipo panopa adakali pa ukaidi umenewu.

Pofuna kuti akhululukidwe ndi kumasulidwa, M’bale Alushkin anakapanga apilo ku Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka. Gululi linapangidwa ndi akatswiri oima paokha omwe amaona za ufulu wa anthu ndipo amagwira ntchito zawo mothandizana ndi nthambi ya bungwe la UN Yoona za Ufulu Wachibadwidwe. Akatswiriwa amaunikanso milandu ya anthu omwe adandaula kuti achitiridwa zinthu zopanda chilungamo monga kutsekeredwa ndi apolisi, kapenanso amene khoti lawagamula kuti akhale pa ukaidi wosachoka panyumba, asungidwe m’ndende milandu yawo isanazengedwe ngakhalenso amene aikidwa m’ndende pambuyo pozenga milandu yawo.

Pambuyo pounikanso bwinobwino zomwe boma la Russia linanena kuti M’bale Alushkin anapalamula mlandu wochita zinthu zoopsa, gululi linalemba kuti: “Bambo Alushkin ankangokambirana ndi anthu mfundo zachipembedzo mwamtendere basi. N’zoonekeratu kuti bambo Alushkin anangogwiritsa ntchito ufulu wawo wopembedza mogwirizana ndi zimene zili mu Gawo 18 la Pangano [Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale, lomwe boma la Russia linasainira kuti ndi membala wake].” Mogwirizana ndi zimenezi, “gululi likufuna kutsindika kuti bambo Alushkin sankayenera kumangidwa komanso kusungidwa m’ndende ndipo bambo Alushkin sakuyenera kuimbidwa mlandu uliwonse.” Komanso, gululi lapempha boma la Russia kuti “lisiyiretu kuchitira bambo Alushkin zinthu zopanda chilungamo,” ndipo gululi likupitirizabe kunena kuti “njira yabwino yothetsera zopanda chilungamozi ndi kutulutsa m’ndende bambo Alushkin mwamsanga.”

Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka, likudziwanso kuti kupatulapo M’bale Alushkin, pali anthu enanso omwe akuvutika chifukwa cha zopanda chilungamo zomwezi. M’baleyu ndi “mmodzi mwa a Mboni za Yehova ambirimbiri m’dziko la Russia omwe akumangidwa, kutsekeredwa m’ndende komanso kuimbidwa milandu chifukwa chongochita zinthu zogwirizana ndi ufulu wawo wopembedza” womwe ndi wovomerezeka ndi malamulo a m’mayiko ena. Choncho pofuna kudzudzula zimene boma la Russia likuchita pozunza abale athu, gululi linanena momveka bwino kuti maganizo akewa sakukhudza mlandu wa M’bale Alushkin wokha, koma akukhudzanso a Mboni za Yehova onse omwe “akukumananso ndi mavuto ofanana ndi a bambo Alushkin.”

Boma la Russia silinachitebe zimene gululi lanena. M’malomwake, akuluakulu a boma la Russia mumzinda wa Penza anapititsa mlandu wa M’bale Alushkin kukhoti mu August 2019. Khotili lakonza zopitiriza kumvetsera mlanduwu pa 15, 19, ndi 22, November 2019.

Pamene tikuyembekezera kuti khoti la ku Russia litsatire maganizo a Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka popereka chigamulo chake chomaliza pa mlandu wa M’bale Alushkin, nafenso tikudalira Yehova mofanana ndi wamasalimo yemwe anati: “Sindidzaopa.  . . . Yehova ali kumbali yanga  . . . Kuthawira kwa Yehova n’kwabwino.”​—Salimo 118:6-9.