Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Kaleriya Mamykina wazaka 78 akuganiziridwa kuti anapalamula mlandu ku Russia chifukwa cha zimene amakhulupirira

JUNE 26, 2019
RUSSIA

Dziko la Russia Likuchitira Nkhanza a Mboni za Yehova Achikulire, Kuphatikizapo Ambiri a Zaka Zoposa 70

Dziko la Russia Likuchitira Nkhanza a Mboni za Yehova Achikulire, Kuphatikizapo Ambiri a Zaka Zoposa 70

M’bale Boris Burylov wazaka 78 akumuganizira kuti anapalamula mlandu wochita zinthu “zoopsa” mumzinda wa Perm’

Mu May 2019, apolisi a m’zigawo za Arkhangel’sk ndi Volgograd ku Russia, anatsegulira milandu alongo athu awiri okalamba. Mlongo Kaleriya Mamykina wazaka 78, yemwe wasonyezedwa pamwambapa, komanso Mlongo Valentina Makhmadgaeva wazaka 71, akunamiziridwa mlandu wochita zinthu “zoopsa” chifukwa choti ndi a Mboni za Yehova.

Mu April 2018, apolisi mumzinda wa Vladivostok anatsegulira mlandu Mlongo Yelena Zayshchuk wazaka 84, limodzi ndi a Mboni enanso 4. Panopa pali abale ndi alongo 10 azaka zoposa 70 omwe apolisi ku Russia akunena kuti anapalamula milandu chifukwa cholambira Yehova.

Ngakhale kuti pa achikulire amenewa palibe yemwe ali m’ndende, n’zosakayikitsa kuti zimene zikuwachitikirazi zikuwasowetsa mtendere kwambiri. Ngati angapitirize kufufuzidwa komanso ngati makhoti angawapeze olakwa, akhoza kuwalipiritsa ndalama zambiri za chindapusa kapena kukawatsekera m’ndende.

Pofika pa 17 June, 2019, chiwerengero cha abale athu omwe akuzengedwa milandu mopanda chilungamo chinali chitafika 215. Chiwerengerochi chikupitirira kukwera. Tisasiye kupempherera abale ndi alongo athu a ku Russia, ndipo nthawi zina tizitchula mayina awo mwachindunji. Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kuwalimbitsa ndi “mphamvu zazikulu chifukwa cha mphamvu zake zaulemerero” kuti athe “kupirira zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe.”—Akolose 1:11.