Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Likulu la bungwe la Federal Service for Financial Monitoring

13 JANUARY 2023
RUSSIA

Dziko la Russia Likupitirizabe Kuika Ziletso pa Nkhani za Ndalama Kwa a Mboni za Yehova Ochuluka

Dziko la Russia Likupitirizabe Kuika Ziletso pa Nkhani za Ndalama Kwa a Mboni za Yehova Ochuluka

Bungwe la Federal Service for Financial Monitoring (Rosfinmonitoring) ndi bungwe la boma lomwe limalimbana ndi umbava pa nkhani za chuma m’dziko la Russia. Mwachitsanzo, limaonetsetsa kuti gulu la anthu ochita zinthu zoopsa lisamalandire ndalama. Limatulutsanso mndandanda wa anthu omwe akuwakayikira kuti ali m’gulu la anthu ochita zinthu zoopsa. Munthu amatha kuikidwa pamndandandawu ngakhale khoti lisanamupeze kuti ndi wolakwa.

Kungoyambira mu 2017 pomwe Khoti Lalikulu Kwambiri la dziko la Russia linaletsa ntchito ya a Mboni za Yehova, mayina 525 a abale ndi alongo akupezeka pamndandandawu. a Chiwerengerochi chikuphatikizapo a Mboni achikulire oposa 100.

Anthu omwe akupezeka pamndandandawu akumawapatsa ziletso pa nkhani ya kagwiritsidwe ntchito ka ndalama. Mwachitsanzo, ma akaunti a kubanki anatsekedwa ndipo banja lililonse likumangololedwa kutengako ndalama zochepa pamwezi pafupifupi madola 137 a ku America kuti lizigwiritsa ntchito pa zinthu zofunika. Iwo akumapatsidwanso ziletso zambiri zomwe zikumapangitsa kuti moyo wawo ukhale wovuta kwambiri. Mwachitsanzo, akumavutika kwambiri kuti agule kapena kugulitsa malo, nyumba kapena galimoto, kupeza inshulansi komanso kulandira ndalama zothandizira anthu amene sali pa ntchito kapenanso kutenga ngongole kubanki. A Mboni omwe anapuma pa ntchito ndi amenenso akumavutika kwambiri chifukwa akumavutika kuti alipire ndalama za kuchipatala komanso nthawi zambiri sakumaloledwa kukwera mabasi kapena magalimoto ena.

M’bale Anton Chermnykh wa ku Ussuriysk yemwe anaikidwa pamndandandawu mu December 2019, ananena kuti: “Kuti ndilandire ndalama yanga ya pa mwezi ndimafunika kupereka umboni wosonyeza kuti sindinazipeze mwachinyengo. Ndinkafunikanso kubweretsa zikalata zambiri kwa ogwira ntchito kubanki kuti azijambule ndi kuzitumiza ku Moscow. Ndipo pamatenga mawiki awiri kuti aone zikalata zonse. Ndiye pa tsiku lomwe asankha, ndimapitanso kubanki ndipo ogwira ntchito kubankiko amatenga ndalama zanga za malipiro ku akaunti n’kundipatsa kenako amatsekanso akaunti yanga nthawi yomweyo. Ogwira ntchito kubanki atsopano akangodziwa zoti ndili pamndandanda wa gulu la anthu ochita zinthu zoopsa, amachita nane mantha.”

Ngakhale kuti abale ndi alongo athu akukumana ndi mavuto onsewa, iwo akupitirizabe kuona zinthu moyenera. M’bale Yuriy Belosludtsev yemwe dzina lake linaikidwanso pamndandandawu zaka ziwiri ndi hafu asanalandire chilango choti azikatsatira malamulo ena ali kunyumba kwake kwa zaka 6, ananena kuti: “Ananditsekera akaunti yanga. Koma ine ndi mkazi wanga tinkathandizidwa ndi abale ndi alongo athu. Tikuyamikira kwambiri Yehova chifukwa cha thandizo lawo.”

Tikudziwa kuti Yehova akuona zinthu zonse zopanda chilungamo zomwe abale ndi alongo athu akupirira ku Russia. Tipitirizabe kupemphera mwachikhulupiriro kuti Yehova apitirize kusamalira abale athu pa nthawi yovutayi.​—Mateyu 6:33.

a Pofika mu December 2022, abale ndi alongo 35 anachotsedwa pamndandanda wa Federal Service for Financial Monitoring pambuyo pomaliza chilango chomwe anapatsidwa kapena kulipira chindapusa.