Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Dmitriy Mikhaylov pamene ankafunsidwa mafunso posachedwapa. Iye anamangidwa ndi akuluakulu a boma la Russia pa 29 May, 2018, ndipo anakhala m’ndende masiku 171

JUNE 18, 2019
RUSSIA

Gulu la Akatswiri a Bungwe la UN Lanena Kuti Dziko la Russia Linaphwanya Malamulo Potsekera M’bale Mikhaylov M’ndende

Gulu la Akatswiri a Bungwe la UN Lanena Kuti Dziko la Russia Linaphwanya Malamulo Potsekera M’bale Mikhaylov M’ndende

Gulu la United Nations la akatswiri oona zamalamulo ochokera m’mayiko osiyanasiyana, lanena kuti zimene dziko la Russia linachita pomanga ndi kusunga m’ndende M’bale Dmitriy Mikhaylov linali “tsankho potengera chipembedzo chake” ndipo dzikoli linaphwanya malamulo omwe mayiko ambiri amatsatira. Akatswiriwa anauzanso dziko la Russia kuti lithetse milandu yonse imene likunena kuti m’baleyu anapalamula.

Gulu la akatswiriwa, lomwe limatchedwa kuti Working Group on Arbitrary Detention, (WGAD) linalemba lipoti la masamba 12 pa nkhani ya M’bale Mikhaylov. Mu lipotilo, gululi linanena kuti zochita za M’bale Mikhaylov “zakhala zili za mtendere nthawi zonse.” Kuonjezera pamenepo, lipotilo linati “palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti a Mikhaylov komanso a Mboni za Yehova ena m’dziko la Russia anachitapo zachiwawa kapena kulimbikitsa anthu ena kuchita zachiwawa.”

Gulu la WGAD linanena kuti M’bale Mikhaylov “anangogwiritsa ntchito ufulu wake wa chipembedzo” ndipo “sanayenere kumangidwa n’kutsekeredwa.” Choncho, akuyenera kupatsidwa chipukutamisozi chifukwa pa nthawi yomwe anali m’ndende sakanatha kugwira ntchito kuti apeze ndalama, komanso chifukwa choti anasungidwa m’ndende ngakhale kuti sanapalamule mlandu uliwonse.

Gulu la WGAD linanenanso kuti kuonjezera pa M’bale Mikhaylov, palinso anthu ena amene akuchitidwa nkhanza chifukwa cha chipembedzo chawo. A Mikhaylov ndi “mmodzi mwa a Mboni za Yehova ambirimbiri m’dziko la Russia amene anamangidwa, kutsekeredwa m’ndende, ndi kuimbidwa mlandu chifukwa chochita zinthu mogwirizana ndi ufulu wachipembedzo,” ufulu womwe ndi wotetezedwa ndi malamulo omwe mayiko ambiri amayendera. Choncho, pofuna kudzudzula mchitidwe wozunza a Mboni za Yehova onse ku Russia, gulu la WGAD linanena momveka bwino kuti zimene zili mu lipoti lawo sikuti zikungokhudza kutsekeredwa m’ndende mopanda chilungamo kwa M’bale Mikhaylov yekha, koma zikukhudzanso a Mboni za Yehova onse amene “akukumana ndi zimene a Mikhaylov akukumana nazo.”

M’bale Mikhaylov anayamba kuphunzira Baibulo ali ndi zaka za pakati pa 13 ndi 19 ndipo anabatizidwa mu 1993, ali zaka 16. Mu 2003, iwo anakwatira Yelena ndipo anayamba kutumikira Yehova limodzi.

Mu 2018, M’bale ndi Mlongo Mikhaylov anazindikira kuti kwa miyezi yambiri apolisi anakhala akujambula mwachinsinsi n’kumamvetsera zimene ankayankhulana ndi anthu ena pafoni komanso ankawajambula pa vidiyo. Pa 19 April, 2018, Komiti Yofufuza Milandu ya Dziko la Russia m’chigawo cha Ivanovo inatsegulira M’bale Mikhaylov mlandu ndipo apolisi onyamula mfuti anapita kunyumba ya m’baleyu kukachita chipikisheni. Patangotha mwezi, m’baleyu anamangidwa n’kutsekeredwa m’ndende chifukwa chomuganizira kuti ankapereka ndalama zothandizira pochita zinthu “zoopsa.” Anakhala m’ndendemo kwa miyezi pafupifupi 6 ndipo kenako anatulutsidwa. Komabe, sakuloledwa kupita kutali komanso apolisi apitiriza kumvetsera mwachinsinsi zimene akuyankhulana ndi anthu ena pafoni pa nthawi yonse imene m’baleyu akhale akufufuzidwa.

Boma la Russia lapatsidwa miyezi 6 kuti liyankhepo pa zimene gulu la WGAD linalemba mu lipoti lake, ndipo bomali likuyenera kuuza gululi ngati lathetsa mlandu wa a Mikhaylov, ngati lawapatsa chipukutamisozi, komanso ngati anthu amene anaphwanya ufulu wa a Mikhaylov afufuzidwa.

Zikuoneka kuti lipoti limene gulu la WGAD linalemba pa mlandu wa M’bale Teymur Akhmedov, lomwe ndi lofanana ndi lipoti lomwe gululi lalemba pa nkhani ya a Mikhaylov, ndi limene linathandiza kuti boma la Kazakhstan litulutse a Akhmedov m’ndende. Mu 2017, a Akhmedov anamangidwa ndipo kenako anagamulidwa kuti akhale m’ndende zaka 5 chifukwa chouza ena zimene amakhulupirira. A Akhmedov ataluza mlanduwu m’makhoti onse a ku Kazakhstan, maloya awo anakadandaula ku gulu la WGAD. Mu lipoti lake la pa 2 October, 2017, gulu la WGAD linadzudzula zimene akuluakulu a boma la Kazakhstan anachita ndipo linauza akuluakuluwa kuti amasule M’bale Akhmedov. Patatha miyezi 6, pulezidenti wa dziko la Kazakhstan anakhululukira a Akhmedov, ndipo anatulutsidwa m’ndende pa 4 April, 2018.

Kaya dziko la Russia litsatira zimene gulu la WGAD lanena pa nkhani ya M’bale Mikhaylov kapena ayi, tikukhulupirira kwambiri lonjezo lakuti: “Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathawira kwa [Yehova].” Tikupemphera kuti Yehova apitirize kusamalira abale ndi alongo athu ku Russia amene akuzengedwa milandu, kuti apitirize kuona kuti anthu onse omwe amakhulupirira Iye molimba mtima “sadzasowa chilichonse chabwino.”—Salimo 34:8, 10.