MAY 18, 2020
RUSSIA
Gulu la Akatswiri a m’Bungwe la UN Lanena Kuti Boma la Russia Linaphwanya Malamulo a Padziko Lonse Pomanga a Mboni 18
Gulu la akatswiri omenyera ufulu wa anthu omwe amagwira ntchito ku bungwe la United Nations latulutsa chikalata cha masamba 15 chosonyeza kuti boma la Russia linaphwanya malamulo pomanga a Mboni za Yehova 18. A Mboniwa anamangidwa m’mizinda yosiyanasiyana kuyambira mu May 2018 mpaka mu July 2019. Akatswiriwa akupempha kuti a Mboni omwe adakali m’ndende atulutsidwe mwamsanga komanso asapatsidwe ziletso zilizonse.
Chikalatachi chinatulutsidwa koyamba pa 15 May 2020. Posachedwapa chikalatachi chidzayamba kupezeka pawebusaiti ya United Nations.
Aka ndi kachitatu kuti Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka lipereke maganizo ake mokomera a Mboni za Yehova. M’chikalatachi, gululi linanena kuti boma la Russia linalakwa pochitira abale ndi alongo athu zinthu zambiri zopanda chilungamo.
Gululi linanenanso kuti panalibe zifukwa zomveka zoti apolisi agwiritse ntchito zida zamphamvu pamene ankamanga a Mboniwa. Akatswiriwa ananenanso kuti “apolisi sankayenera kumanga [a Mboniwa] n’kukawatsera m’ndende ndiponso sankayenera kapenanso sakuyenera kuwazenga mlandu uliwonse.”
Gululi latsutsa zoti a Mboniwa anapalamula mlandu wochita zinthu zoopsa. Lafotokozanso kuti abale ndi alongowa ankangogwiritsa ntchito “ufulu wawo wopembedza mwamtendere.”
M’chikalatachi, akatswiriwa anadzudzula zimene khoti linachita pa nthawi yozenga milandu ya abale ndi alongowa. Mwachitsanzo, alongo awiri anawaika m’chipinda china cha khoti chotchinga ndi zitsulo pa nthawi yomvetsera milandu yawo. Malinga ndi zimene zili m’chikalatachi, malamulo a padziko lonse amanena kuti munthu aliyense ali ndi ufulu “woonedwa kuti ndi wosalakwa pokhapokha ngati khoti lapeza kuti ndi wolakwa.” Potengera zimenezi, khotilo silinafunike “kumanga ndi unyolo kapenanso kuwaika alongowa m’chipinda chotchinga ndi zitsulo pamene linkawazenga milandu ndiponso silinayenere kuwachitira zinthu ngati kuti ndi zigawenga zoopsa.”
Gululi lapemphanso boma la Russia kuti litseke milandu yonse yomwe a Mboni 18 akuimbidwa komanso liwapatse chipukuta misozi mogwirizana ndi zimene zili m’malamulo a padziko lonse. Ndiponso dzikoli likupemphedwa kuti “lifufuze zinthu zopanda chilungamozi mokwanira komanso mosakondera” ndipo “lichitepo kanthu poonetsetsa kuti aliyense amene anaphwanya ufulu wa [a Mboniwa] walandira chilango choyenerera.”
Chikalata chochokera ku gululi chikusonyezanso kuti a Mboni 18 amenewa ali “m’gulu la a Mboni za Yehova ambiri omwe anamangidwa, kutsekeredwa m’ndende komanso kuimbidwa milandu yochita zoopsa ngakhale kuti ankangogwiritsa ntchito ufulu wawo wopembedza basi.” Dziko la Russia linasainira nawo pangano loti lizilemekeza ufuluwu pamodzinso ndi mayiko ena. Potengera zimenezi, mfundo zomwe zikupezeka m’chikalatachi “zikugwiranso ntchito kwa anthu onse omwe achitiridwa zopanda chilungamo ngati zimenezi.”
Zimene zili m’chikalatachi sikuti zikutsimikizira zoti abale ndi alongo athu ku Russia atulutsidwa m’ndende, komabe tikukhulupirira kuti zikhoza kuthandiza kuti zinthu zisinthe. Panopa tikudikira kuti tione zimene dziko la Russia liyankhe pa nkhaniyi. Popeza kuti abale ndi alongo athu ku Russia amadalira Yehova, yemwe ndi Atate wathu, ndiponso akusonyeza kulimba mtima popirira chizunzo, tikudziwa kuti Iye apitirizabe kuwathandiza kuti akhale achimwemwe komanso mwamtendere.—Aroma 15:13.