Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

12 MAY 2021
RUSSIA

Khoti Lakana Apilo ya Mlongo Svetlana Monis

Khoti Lakana Apilo ya Mlongo Svetlana Monis

Pa May 12, 2021, khoti la ku Russia linakana apilo ya Mlongo Monis. Khotili linapereka chigamulo chokomera woimira boma pa mlanduwu choti asinthe chilango cha mlongoyu. Choncho anasintha kuti m’malo moti apereke chindapusa cha marubo 10,000 (madola 135 a ku United States), akhale pa ukaidi wa zaka ziwiri ndi hafu koma asapite kundende panopa.