Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Sergey Klimov ali muselo ya m’khoti mu May 2019

NOVEMBER 11, 2019
RUSSIA

Khoti Lapereka Chigamulo Chowawa Kwambiri kwa M’bale Klimov ku Russia

Khoti Lapereka Chigamulo Chowawa Kwambiri kwa M’bale Klimov ku Russia

Pa 5 November, 2019, Khoti la m’boma la Oktyabrsky mumzinda wa Tomsk linagamula kuti M’bale Sergey Klimov akhale m’ndende kwa zaka 6. A Dennis Christensen ndi m’bale winanso ku Russia yemwe anagamulidwa kukhala m’ndende kwa nthawi yaitali chonchi. Komabe, popereka chigamulo pa mlandu wa M’bale Klimov, khoti linaonjezera zinthu zinanso zambiri zomwe M’baleyu sakuloledwa kuchita. Choncho chigamulochi ndi chowawa kwambiri pa zigamulo zomwe abale athu apatsidwa kungochokera pamene Khoti Lalikulu Kwambiri linaletsa ntchito yathu mu 2017.

M’bale Klimov anamangidwa pa 3 June, 2018, pa nthawi yomwe apolisi komanso asilikali anakachita chipikisheni m’nyumba ziwiri za a Mboni za Yehova. Abale ndi alongo 30 kuphatikizapo mlongo wazaka 83 anatengedwa kuti akafunsidwe mafunso. Ena onse anawasiya kuti azipita kupatulapo M’bale Klimov. M’baleyu anauzidwa kuti anapalamula mlandu ndipo khoti linagamula kuti akhale m’ndende kwa miyezi iwiri poyembekezera kuzenga mlandu wake. Asanapatsidwe chigamulo choti akhale m’ndende kwa zaka 6, M’bale Klimov wakhala akusungidwa m’ndende kwa chaka ndi miyezi 5 mlandu wake usanazengedwe. Pa nthawiyi sanaloledwe kuonana ndi mkazi wake komanso achibale ake.

Maloya a M’bale Klimov akapanga apilo chigamulochi. Komanso, pa 20 August, 2018, anakadandaula zokhudza chigamulochi (Klimov v. Russia) ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe.

Abale athu ku Russia akhala akumangidwa, kusungidwa m’ndende komanso nyumba zawo zakhala zikuthyoledwa ndi apolisi ndipo zimenezi zakhala zikuwonjezeka kwambiri m’chaka chonse cha 2019. Koma abale athuwa akhalabe okhulupirika komanso olimba mtima. Timalimbikitsidwa kwambiri tikaona umboni wosonyeza kuti Yehova akudalitsa abale athuwa chifukwa choti akumudalira ndi mtima wawo wonse.​—Salimo 56:1-5, 9.