Pitani ku nkhani yake

MARCH 20, 2019
RUSSIA

Khoti Latulutsa M’ndende M’modzi Mwa a Mboni Atatu Omwe Anamangidwa Mumzinda wa Surgut ku Russia

Khoti Latulutsa M’ndende M’modzi Mwa a Mboni Atatu Omwe Anamangidwa Mumzinda wa Surgut ku Russia

Pa 7 March, 2019, Khoti la Apilo ku Khanty-Mansiysk m’dziko la Russia, linasintha chigamulo chomwe khoti la mumzinda wa Surgut linapanga choti M’bale Artur Severinchik aikidwe m’ndende. M’baleyu anatulutsidwa m’ndende pa 15 March.

A Severinchik ndi m’modzi mwa abale atatu omwe anaikidwa m’ndende pa 17 February poyembekezera kuwazenga milandu. Iwo anawamanga pa nthawi imene apolisi ankathyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni m’mizinda ya Surgut komanso Lyantor. Koma khotili lakana kutulutsa abale ena awiri omwe mayina awo ndi a Yevgeniy Fedin komanso a Sergey Loginov.

Zomwe zachitikazi zachititsa maboma komanso ofalitsa nkhani kuti akhale ndi chidwi ndi nkhaniyi. Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linalamula kuti M’bale Loginov aunikidwe ndi madokotala omwe sagwira ntchito m’zipatala za boma. M’baleyu anachitidwa zankhanza pa nthawi imene anaikidwa m’ndende.

Tikuthokoza kuti M’bale Severinchik anatulutsidwa m’ndende. Tipitirizabe kupemphera kuti abale athu omwe ali m’ndende ku Russia azidalira Yehova komanso azikumbukira kuti iye awathandiza kuti ‘asagwedezeke.’—Salimo 16:8.