Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JANUARY 31, 2019
RUSSIA

Khoti Ligamula Mlandu wa a Dennis Christensen pa 6 February, 2019

Khoti Ligamula Mlandu wa a Dennis Christensen pa 6 February, 2019

Khoti la m’Boma la Zheleznodorozhniy ku Oryol lamaliza kuzenga mlandu wa a Dennis Christensen, ndipo woweruza mlanduwu wanena kuti adzapereka chigamulo chake Lachitatu, pa 6 February, 2019.

M’bale Christensen wakhala ali m’ndende kungoyambira pamene anamangidwa pa 25 May, 2017. Iwo anayamba kuzengedwa mlandu pa 19 February, 2018. Ngati atapezeka wolakwa, maloya omwe anakasuma mlandu wa M’bale Christensen apempha kuti adzakhale m’ndende kwa zaka 6 ndi hafu.

Ngakhale kuti M’bale Christensen wakhala m’ndende kwa miyezi yoposa 20, iye akusangalalabe, akudalira Yehova ndipo akuyamikira kwambiri mapemphero omwe abale padziko lonse akupereka.—2 Atesalonika 3:1, 2.