Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

7 MARCH, 2022
RUSSIA

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Lati Boma la Russia Linaphwanya Ufulu wa Mboni za Yehova

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Lati Boma la Russia Linaphwanya Ufulu wa Mboni za Yehova

Pa 22 February 2022, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linapereka zigamulo ziwiri mokomera a Mboni za Yehova okwana 15. Zigamulozi zinaperekedwa pa milandu yokhudza apolisi omwe anazunza abale athu pa nthawi imene apolisiwo ankafufuza zinthu m’nyumba zawo, kuyambira mu 2010 mpaka mu 2012. Zigamulozo zasonyeza kuti boma la Russia linaphwanyira abale ndi alongo athu ufulu wawo wachipembedzo. Boma la Russia aligamula kuti lilipire chipukuta misozi cha ndalama zokwana madola 112,323 a ku United States. Zigamulozi ndi zomaliza ndipo boma la Russia silingaloledwe kupanga apilo.

Zigamulo ziwiri zomwe zaperekedwazi, zikugwira ntchito pa milandu yokwana 6 yomwe abale anasumira boma la Russia. a Milanduyi inali yofuna kupeza ngati kunalidi koyenera kuti apolisi a boma la Russia apatsidwe chilolezo chokafufuza zinthu m’nyumba za Mboni za Yehova komanso m’Nyumba ya Ufumu. Amaunikanso kuti aone ngati zinali zoyenera kuti apolisiwo avule ndi kusecha alongo athu awiri omwe anawamanga atawapeza akulalikira, komanso ngati kunalidi koyenera kuti awalande katundu. Nthawi zina pofufuza zinthu m’nyumba za abale, kunkabwera apolisi a FSB omwe ankakhala ndi mfuti komanso atadziphimba kunkhope. Apolisiwa ankachitira nkhanza abale ndi alongo athu.

Pothirirapo ndemanga pa kufunika kwa zigamulozi, André Carbonneau yemwe ndi loya woona za ufulu wa anthu padziko lonse, amenenso anapemphedwa ndi dipatimenti yathu yoona zamalamulo kuti athandizepo pankhanizi, anafotokoza kuti zigamulozi, “zikusonyeza poyera kuti boma la Russia linkachita zinthu mopanda chilungamo ndipo linkaphwanya malamulo pokafufuza zinthu m’nyumba za Mboni za Yehova. Izi zikuphatikizapo ntchito yokafufuza zinthu m’nyumba zokwana 1,700 yomwe inachitika pambuyo potseka ntchito za Mboni za Yehova mu 2017. Moti ngati panopo apolisi angakafufuzenso zinthu m’nyumba ya aliyense chifukwa choti munthuyo ndi wa Mboni za Yehova, akhala akuphwanya malamulo komanso mfundo zomwe mayiko a ku Europe anagwirizana.” Iye anawonjezeranso kuti: “Muyeneranso kudziwa kuti khotili ladzudzula akuluakulu a boma la Russia chifukwa choletsa ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba. Izi zikusonyeza kuti Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe limaona kuti kulalikira ndi mbali ya ntchito zachipembedzo zomwe akuluakulu a boma sayenera kusokoneza.”

Ngakhale kuti zigamulozi sizikudzudzula zinthu zankhanza zimene a Mboni za Yehova akukumana nazo ku Russia, komabe zithandiza pa nkhani yoona ngati kunalidi koyenera kuti boma liletse ntchito zagulu lathu. Pali milandu inanso yokwana 60 yomwe a Mboni za Yehova ku Russia anakasuma ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe. Tikukhulupirira kuti zigamulo ziwiri zomwe zaperekedwazi zatipatsa chithunzithunzi cha mmene milandu inayo idzagamulidwire.

Tikusangalala kwambiri kuona kuti akuluakulu oona za ufulu wa anthu aona kukhulupirika komwe abale ndi alongo a ku Russia asonyeza. Zigamulo zomwe zaperekedwazi, ndi umboni woti Yehova akudalitsa abale athu chifukwa cha kukhulupirika kwawo poteteza dzina lake komanso chifukwa chokhala okhulupirika ku ulamuliro wake.—Salimo 26:11.

a Milandu 6yo inkadziwika motere: Mlandu wa Chavychalova wosumira boma la Russia; Mlandu wa Cheprunovy ndi Anzake Wosumira Boma la Russia; Mlandu wa Novakovskaya Wosumira Boma la Russia; Mlandu wa Ogorodnikov ndi Anzake Wosumira Boma la Russia; Mlandu wa Pekshuyev ndi Anzake Wosumira Boma la Russia; komanso Mlandu wa Zharinova Wosumira Boma la Russia.