Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MARCH 1, 2019
RUSSIA

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Layankha Mwamsanga Pempho Lokhudza M’bale Yemwe Anachitidwa Nkhanza ku Russia

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Layankha Mwamsanga Pempho Lokhudza M’bale Yemwe Anachitidwa Nkhanza ku Russia

Pa 25 February, 2019, maloya a M’bale Sergey Loginov anapempha Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe kuti lichitepo kanthu mwamsanga pofuna kuteteza m’bale wathuyu. Iye ndi mmodzi mwa abale 7 omwe anachitidwa nkhanza ndi apolisi kumadzulo kwa mzinda wa Surgut ku Siberia. Abale ena 6 omwe anachitidwa nkhanza amasulidwa, koma M’bale Loginov wakhala akusungidwa m’ndende kuchokera pamene anamangidwa ndipo atavulazidwa sanalandire thandizo la mankhwala lokwanira.

Pa 26 February, patangodutsa tsiku limodzi kuchokera pamene pempholi linaperekedwa, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linapereka chigamulo chokomera M’bale Loginov. Khotili linagwirizana ndi zimene maloya a M’bale Loginov anapempha, ndipo linalamula boma la Russia kuti m’baleyu awunikidwe “mwamsanga” ndi madokotala omwe sagwira ntchito m’zipatala za boma, kuti aone mmene thupi lake linavulalira komanso mmene nkhanzazi zinamusokonezera maganizo. Khotilo linanenanso kuti madokotalawo aone ngati thanzi la m’baleyu lili bwino moti akhoza kukhalabe m’ndende. Boma la Russia likuyenera kutsatira zimene khotili lalamula pofika pa 11 March, 2019.

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe limavomera mapempho ngati amenewa n’zochitika zovuta kwambiri zokha, ngati likuona kuti munthu angavulazidwe m’njira yoti akhoza kumakhala movutika kwa moyo wake wonse. Choncho n’zolimbikitsa kuti khotili linachitapo kanthu mwamsanga, patangodutsa tsiku limodzi kuchokera pamene pempholi linaperekedwa. Khotili lanena kuti lizitsatira mwachidwi komanso kulemba nkhani zokhudza nkhanza zomwe abale athu akukumana nazo.

Panopa, a Mboni 19 akuimbidwa milandu mumzinda wa Surgut ndipo atatu mwa a Mboniwa akuwasunga m’ndende poyembekezera kuwazenga milandu.

Pamene tikupitiriza kupemphera kwa Yehova mopembedzera m’malo mwa abale athuwa, tiyeni tiziganizira kwambiri mawu olimbikitsa opezeka m’buku la Yeremiya, akuti: “Wodala ndi munthu aliyense amene amakhulupirira Yehova, amene amadalira Yehova.”—Yeremiya 17:7.