Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

SEPTEMBER 25, 2020
RUSSIA

Khoti ku Russia Lagamula Kuti Banja la a Bazhenov Ndiponso Mlongo Wazaka 73 Azitsatira Malamulo Ena Ali Kunyumba Kwawo

Khoti ku Russia Lagamula Kuti Banja la a Bazhenov Ndiponso Mlongo Wazaka 73 Azitsatira Malamulo Ena Ali Kunyumba Kwawo

Pa 25 September 2020, khoti la m’boma la Yelizovsky m’dera la Kamchatka linapereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Konstantin Bazhenov, mkazi wake Snezhana ndiponso Mlongo Vera Zolotova. Poyamba woimira boma pamlanduwu ankafuna kuti khoti lilipiritse M’bale ndi Mlongo Bazhenov chindapusa cha ndalama zokwana madola 7,850 a ku America ndipo Mlongo Zolotova ndalama zokwana madola 5,195 a ku America. Koma khoti linagamula kuti onsewa azikatsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo kwa zaka ziwiri ndipo pambuyo pake adzaletsedwa kuchitanso zinthu zina kwa miyezi 6. M’bale ndi Mlongo Bazhenov komanso Mlongo Zolotova akusangalala kuti sapita kundende kapenanso kulipira chindapusa.