Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Yuriy Zalipayev akufotokoza mawu ake omaliza m’khoti

OCTOBER 7, 2020
RUSSIA

Khoti ku Russia Lagamula Kuti M’bale Yuriy Zalipayev Ndi Wosalakwa

Khoti ku Russia Lagamula Kuti M’bale Yuriy Zalipayev Ndi Wosalakwa

Pa 7 October 2020, khoti la m’boma la Mayskiy ku Kabardino-Balkarian Republic linaweruza kuti M’bale Yuriy Zalipayev sanapalamule mlandu uliwonse. Maloya oimira boma pamlanduwu angathe kupanga apilo m’masiku 10 akubwerawa.

Oimira boma pamlanduwu ankanena kuti M’bale Zalipayev anapalamula mlandu wolimbikitsa anthu ena kuchita zachiwawa. Koma popereka umboni pa nkhaniyi, anthu oposa 30 anatsutsa zimenezi. Iwo ananena kuti m’baleyu ankangolimbikitsa anthu kuwerenga Baibulo komanso kuti azisonyeza chikondi ndi kuchitira chifundo anthu onse.

Komanso khotili linapereka chigamulochi potengera zimene Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka linanena posachedwapa kuti a Mboni za Yehova sachita zachiwawa kapena kulimbikitsa anthu ena kuchita zimenezo ngakhale pang’ono.

Khoti litangolengeza za chigamulochi, M’bale Zalipayev ananena kuti: “Anthu a m’banja langa komanso anzanga anali okonzeka kumva za chigamulo chilichonse chokhwima chimene ndikanapatsidwa. Ndikuthokoza kwambiri Yehova kuti ndinalibe mantha pa nthawi imene mlandu wanga unkazengedwa. Ndine wosangalala ndipo ndikuthokoza kwambiri onse amene anaperekera umboni woti ndine wosalakwa.”