Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

May 23, 2019
RUSSIA

Khoti la Apilo Lagwirizana ndi Chigamulo Choti a Dennis Christensen Amangidwe

Khoti la Apilo Lagwirizana ndi Chigamulo Choti a Dennis Christensen Amangidwe

Pa 23 May, 2019, oweruza atatu a khoti la m’chigawo cha Oryol anakana apilo imene a Dennis Christensen anapanga ndipo khotili linagwirizana ndi chigamulo cha poyamba choti a Christensen akakhale m’ndende zaka 6. Abale ndi alongo athu pafupifupi 80 anali nawo kukhotiko kukamvetsera mlanduwu. Akuluakulu a boma ochokera ku Australia ndi ku Denmark analiponso pa tsiku lozenga mlanduwu. Ofalitsa nkhani a mayiko ena ayamba kale kulengeza za chigamulochi.

Pa miyezi itatu yapitayi kuchokera mu February pomwe M’bale Christensen anagamulidwa kuti akakhale m’ndende, nyumba za abale zokwana 115 zinathyoledwa ndipo boma linatsegulira milandu a Mboni za Yehova ambiri poyerekezera ndi mmene zinalili miyezi ina itatu yapitayo.

Tikupempherera M’bale Christensen komanso okhulupirira anzathu onse ku Russia. Sitikukayika kuti Yehova “ali pafupi ndi onse oitanira pa iye” ndipo apitirizabe kuthandiza abale athu amene akupitirizabe kukhala okhulupirika ngakhale kuti akuzunzidwa—Salimo 145:18.