Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

25 JANUARY 2021
RUSSIA

Khoti la Apilo ku Russia Lagwirizana Ndi Chigamulo Choti M’bale Zalipayev Ndi Wosalakwa

Khoti la Apilo ku Russia Lagwirizana Ndi Chigamulo Choti M’bale Zalipayev Ndi Wosalakwa

Pa 25 January 2021, Khoti Lalikulu Kwambiri ku Kabardino-Balkarian Republic linakana apilo ya oimira boma pa mlandu yopempha kuti chigamulo cha pa 7 October 2020 chisinthidwe. Chigamulochi chinanena kuti M’bale Yuriy Zalipayev ndi wosalakwa. Oimira boma pa mlandu angasankhe kupanga apilo chigamulo chatsopanochi. Komabe, chigamulo chatsopanochi chayamba kale kugwira ntchito ndipo khoti lathetsa milandu yonse yomwe M’baleyu amaimbidwa. Panopa M’bale Zalipayev ali ndi ufulu wopempha chipepeso chifukwa choimbidwa mlandu wabodza.

M’bale Zalipayev ankakhulupirira Yehova komanso ankachita zinthu molimba mtima m’khoti ngakhale kuti ankadziwa kuti chigamulo choti ndi wosalakwa chikhoza kusinthidwa. Khoti litangotsala pang’ono kupereka chigamulochi M’bale Zalipayev anauza khotilo molimba mtima kuti posachedwapa Mulungu adzathetsa zoipa zonse kuphatikizapo kuzunzidwa kwa a Mboni za Yehova ku Russia. Iye anati: “Ngakhale kuti ozunzawa akuyesetsa kugwiritsa ntchito njira zooneka ngati zapamwamba kwambiri, koma pali chinthu chimodzi chimene ayenera kudziwa. Sangakwanitse kugwiritsa ntchito njira zawozi pofuna kuti ndisiye kukhulupirira malonjezo a Mulungu akuti posachedwapa adzathetsa zoipa zonse padzikoli. Ndili ndi chikhulupiriro kuti posachedwapa tidzaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo lakuti anthu amitundu yosiyanasiyana adzazindikira kuti ndi anthu a m’banja limodzi logwirizana. Palibe chimene chingadzasokoneze mgwirizanowu. Ponena za Mulungu, Baibulo limati: ‘Mulungu adzakhala woweruza pakati pa mitundu ndipo adzakonza zinthu zokhudza mitundu yambiri ya anthu. Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo. Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.’”​—Yesaya 2:4.

Iye anamaliza ndi kunena kuti: “Ndikukhulupirira ndi mtima wonse kuti lonjezoli latsala pang’ono kukwaniritsidwa.”