Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Yevgeniy Spirin ndi mkazi wake Natalya

OCTOBER 14, 2020
RUSSIA

Khoti la Apilo ku Russia Lagwirizana Ndi Zoti M’bale Spirin Ndi Wolakwa Ndipo Apereke Chindapusa

Khoti la Apilo ku Russia Lagwirizana Ndi Zoti M’bale Spirin Ndi Wolakwa Ndipo Apereke Chindapusa

Pa 14 October 2020, Khoti la M’chigawo cha Ivanovo linagwirizana ndi chigamulo chimene M’bale Yevgeniy Spirin anapatsidwa mu July 2020. Khoti la apilo la m’chigawochi linakana zimene oimira boma pamlanduwu ananena zoti mlandu wa M’bale Spirin ubwererenso kukhoti. N’zosakayikitsa kuti oimira boma pamlanduwu achita apilo yopempha khoti kuti M’baleyu akakhale kundende zaka 7 ngati mmene anapemphera poyamba.