Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 31, 2021
RUSSIA

Khoti la Russia Lakana Apilo ya a Mboni za Yehova Okwana 4

Khoti la Russia Lakana Apilo ya a Mboni za Yehova Okwana 4

Pa 28 May 2021, Khoti la M’chigawo cha Omsk linakana apilo ya M’bale Sergey Polyakov ndi mkazi wake Anastasia, Mlongo Gaukhar Bektemirova komanso Mlongo Dinara Dyusekeyeva. M’bale Polyakov apitirizabe kukhala m’ndende pomwe alongo atatuwa azingotsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo.