Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

27 JANUARY, 2020
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’bale Aleksandr Prianikov, Mlongo Venera Komanso Mlongo Darya Dulova Ndi Olakwa

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’bale Aleksandr Prianikov, Mlongo Venera Komanso Mlongo Darya Dulova Ndi Olakwa

Pa 27 January 2020, khoti lamumzinda wa Karpinsk linagamula kuti M’bale Aleksandr Prianikov, limodzi ndi alongo awiri omwe mayina awo ndi Venera komanso Darya Dulova, ndi olakwa. M’bale Aleksandr Prianikov anauzidwa kuti asapezekenso ndi mlandu kwa zaka ziwiri ndi hafu. Mlongo Venera anauzidwa kuti asapezekenso ndi mlandu wina kwa zaka ziwiri ndipo Mlongo Darya anauzidwa kuti asapezekenso ndi mlandu wina kwa chaka chimodzi. Onsewa anauzidwa kuti ngati atalephera kuchita zimenezi, adzatsekeredwa m’ndende kwa nthawi yofanana ndi imene auzidwayo. Anthu atatuwa achita apilo mlanduwu kukhoti lina.