Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Aleksandr Shcherbina

APRIL 6, 2021
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’bale Aleksandr Shcherbina Akakhale M’ndende kwa Zaka Zitatu

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’bale Aleksandr Shcherbina Akakhale M’ndende kwa Zaka Zitatu

Chigamulo

Pa 6 April 2021, khoti la ku Abinskiy ku Krasnodar linapereka chigamulo pa mlandu wa M’bale Aleksandr Shcherbina ndipo linagamula kuti akakhale m’ndende kwa zaka zitatu. Pochoka ku khotiko m’baleyu anamutengera kundende nthawi yomweyo muselo. Iye apanga apilo chigamulochi.

Zokhudza M’baleyu

Aleksandr Shcherbina

  • Chaka chobadwa: 1976 (ku Kholmskaya, Krasnodar)

  • Mbiri yake: Makolo ake onse anamwalira. Iye anagwirapo ntchito ngati dalaivala wa thiraki, wokonza magalimoto komanso kalipentala.

  • Ali wachinyamata ankakonda kusewera basketball komanso mpira. Anaphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ali ndi zaka za m’ma 20. Ataphunzira za maulosi amene anakwaniritsidwa anayamba kukhulupirika kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu ndipo mu 1999 anabatizidwa.

Mlandu Wake

Akuluakulu a boma ku Krasnodar anakachita chipikisheni m’nyumba mwa M’bale Aleksandr Shcherbina kawiri, mu April ndi mu December 2020. Pa maulendo onsewa, Aleksandr ankafunsidwa mafunso ndi apolisi ndipo anamulanda Baibulo komanso zipangizo zake zamakono.

Mlandu wa M’baleyu unayamba pa 17 March 2021, kukhoti la ku Abinskiy. Mofanana ndi milandu ya abale ena imene inazengedwa mukhotili, mlandu wa Aleksandr unazengedwa mofulumira kwambiri.

Ali mukhoti, Aleksandr ananena molimba mtima kuti: “Zoona n’zakuti ndikuimbidwa mlandu chifukwa chakuti ndimakhulupirira Mulungu komanso ndikupitirizabe kukhala wa Mboni za Yehova. Zimenezi zikutanthauza kuti ndikuimbidwa mlandu chifukwa chogwiritsa ntchito ufulu wanga womwe ndi wogwirizana ndi Gawo 28 la Malamulo Oyendetsera Dziko la Russia. Zimene chipembedzo changa chimakhulupirira ndi zogwirizana ndi Baibulo. Choncho ndi zosiyana kwambiri ndi zimene zimatchulidwa kuti zinthu zoopsa.”

Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa cha abale ndi alongo athu a ku Russia omwe akupitirizabe kukhala zitsanzo zabwino pa nkhani ya kulimba mtima komanso kukhulupirika. Ndipo tikudziwa kuti Yehova adzawadalitsa kwambiri chifukwa chopirira pamene akuchita “chifuniro cha Mulungu.”—Aheberi 10:36.