Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Khasan Kogut ndi mkazi wake Yekaterina, pambuyo pa chigamulo

SEPTEMBER 10, 2020
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’bale Khasan Kogut Ndi Wolakwa

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’bale Khasan Kogut Ndi Wolakwa

Pa 10 September 2020, Khoti la Mumzinda wa Berezovsky m’Chigawo cha Kemerovo linagamula kuti M’bale Khasan Kogut ndi wolakwa. M’baleyu anapatsidwa chilango cha zaka ziwiri ndi hafu koma sakakhala kundende. M’malomwake, anapatsidwa malamulo oti aziyendera pa zaka zimenezi. Khotili linagamulanso kuti aletsedwe kuchita zinthu zina kwa zaka zinanso ziwiri. M’bale Kogut akusangalala kuti saikidwa m’ndende ndipo apitirizabe kukhala ndi mkazi wake komanso mwana wake wazaka 8.