Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

4 FEBRUARY, 2020
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’bale Kim ndi Polevodov Ndi Olakwa

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’bale Kim ndi Polevodov Ndi Olakwa

Pa 4 February 2020, khoti la mumzinda wa Zheleznodorozhniy ku Khabarovsk linagamula kuti M’bale Stanislav Kim komanso Nikolay Polevodov ndi olakwa. Abalewa anauzidwa kuti asapite kundende koma azitsatira malamulo enaake kwa zaka ziwiri. Iwo adzachita apilo chigamulochi. Abalewa akuimbidwanso mlandu pa nkhani ina kukhoti lina la mumzindawu. Tsiku lopereka chigamulo pamlanduwo silinakhazikitsidwe.