Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Ruslan Alyev ndi mkazi wake Krisina ali panja pa khoti pa 17 December 2020

DECEMBER 17, 2020
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’bale Ruslan Alyev Azitsatira Malamulo Ena Ali Kunyumba

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’bale Ruslan Alyev Azitsatira Malamulo Ena Ali Kunyumba

M’nkhaniyi mulinso zimene M’bale Alyev ananena

Pa 17 December 2020, Khoti la m’Boma la Leninskiy ku Rostov-on-Don linagamula kuti M’bale Ruslan Alyev ndi wolakwa ndipo linalamula kuti azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwake kwa zaka ziwiri ndi hafu. Panopa sakuyenera kukakhala kundende.

Pa nthawi imene ankayembekezera tsiku loti khoti lipereke chigamulo, M’bale Alyev anasonyeza kuti ali ndi “mtendere wa Mulungu.” (Afilipi 4:7) Iye anauza anzake modekha kuti: “Sindikuda nkhawa ndi zilizonse zimene khoti lingagamule. Mulungu sangandisiye ndekha pa zilizonse zimene angalole kuti zindichitikire ndipo ndikukhulupirira kuti adzandithandiza pa nthawi yake yoyenera. Sindidzasiya kutumikira Yehova kulikonse kumene ndingakhale.” M’bale Alyev akudziwanso kuti abale ndi alongo padziko lonse akhala akumupempherera kuti akwanitse kupirira mokhulupirika ndipo iye akuti mapemphero amenewo “amutonthoza kwambiri.”

M’mawu ake omaliza omwe ananena m’khoti pa 14 December, 2020 M’bale Alyev ananena kuti: “Zaka 2,000 zapitazo mnyamata wina wazaka 33 ankaimbidwa mlandu woukira boma ndipo anagamulidwa ngati chigawenga. Koma maumboni okhudza mlandu wakewo akusonyeza kuti anazunzidwa chifukwa chakuti ankatumikira Yehova Mulungu. Anthu amene ankaperekera umboni pa mlandu wake ankangokolanakolana ndipo zinkavuta kumupeza kuti ndi wolakwadi. Komabe khoti linagamula kuti ndi wolakwa. Munthu ameneyu ndi Yesu Khristu.”

M’bale Alyev anapitiriza kunena kuti: “Ndiye lero, pambuyo pa zaka 2,000 chichitikireni nkhaniyi, inenso ndine mnyamata wazaka 33 ndipo ndili m’khoti kuimbidwa mlandu woukira boma komanso kuti ndikuika pachiopsezo chitetezo cha dziko. . . . Ndikamamva zimenezi ndikudabwa kwambiri poona kuti mlandu umene ndikuimbidwawu ndi wabodza.”

M’bale Alyev anafotokozanso kuti si zoona kuti iyeyo amalimbikitsa anthu ena kuti azidana ndi zipembedzo zina. Iye anati: “Pa zifukwa zosiyanasiyana, ndinakula ndi anthu azikhalidwe zitatu: Chirasha, Chiazebaijani ndiponso Chiyukireni. Ineyo ndimakonda anthu azikhalidwe zonsezi. . . . Ndilinso ndi anzanga ambiri omwe amachokera m’mayiko a ku Africa omwe amayankhula Chingelezi komanso oyankhula Chitchainizi. . . . Ndinabadwira ku Azerbaijani. Aliyense amadziwa bwino kuti anthu a ku Azerbaijan amadana ndi anthu a ku Armenia, koma ine ndili ndi mnzanga wa ponda apa m’pondepo yemwe ndi wa ku Armenia. Mnzangayu anabweranso pa ukwati wanga. Ndimakonda anthu omwe ndimasiyana nawo mitundu, zikhalidwe, zipembedzo komanso zokonda chifukwa cha zimene ndimaphunzira m’chipembedzo changa. . . . Ndipo panopa ineyo komanso anthu omwe amandidziwa bwino tikudabwa kwambiri kuti mlandu umene ndikuzengedwa ndi wokhudza kudanitsa anthu a mitundu ndi zikhalidwe zina komanso wakuti ndimalimbikitsa anthu ena kudziona kuti ndi apamwamba kuposa ena.”

N’zolimbikitsa kumva kuti abale ndi alongo athu ku Russia akuyesetsa kugwiritsa ntchito nthawi yomwe akuzengedwa mlandu m’khoti polalikira. Sitikukayikira kuti Yehova adalitsa mbewu za choonadi zomwe tikudzala tikamatofokozera akuluakulu aboma zomwe timakhulupirira.—Mateyu 10:18.