Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 24, 2020
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’bale Sergey Ledenyov Azitsatira Malamulo Ena Ali Kunyumba kwa Zaka Ziwiri

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’bale Sergey Ledenyov Azitsatira Malamulo Ena Ali Kunyumba kwa Zaka Ziwiri

Pa 24 November 2020, Khoti la Mumzinda wa Petropavlovsk-Kamchatskiy m’Chigawo cha Kamchatka linagamula kuti M’bale Sergey Ledenyov ndi wolakwa. Khotili linagamula kuti m’baleyu azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwa zaka ziwiri ndiponso aziyang’aniridwa kwa zaka zitatu ndi apolisi amene amayang’anira anthu opalamula milandu. Panopa sakuyenera kupita kundende.

Pa tsiku lomaliza limene khoti linkazenga mlandu wawo, a Ledenyov anafotokoza molimba mtima zimene kukhala wa Mboni za Yehova kumatanthauza. Iwo anati: “Dzina lakuti Yehova si dzina la munthu, chipembedzo kapena la gulu linalake koma ndi dzina lenileni la Mulungu. M’Baibulo, m’buku la mneneri Yesaya, Yehova amatchula atumiki ake kuti ‘mboni zanga.’ Mogwirizana ndi mawu amenewa, pamsonkhano umene unachitika mu 1931, tinayamba kudziwika ndi dzina lakuti ‘Mboni za Yehova.’ Anthu amene amadziwika ndi dzinali amayenera kuchitira umboni za Mulungu kutanthauza kuti ayenera kuuza ena zokhudza iyeyo monga Mlengi, Mpulumutsi komanso Woyenera kulamulira chilengedwe chonse ndiponso kuuza ena zokhudza zinthu zabwino zimene Mulungu wakonzera anthu. Umenewu ndi mwayi wapadera kwambiri umene ineyo ndi Akhristu anzanga onse tili nawo.”—Yesaya 43:10.

A Ledenyov anauzanso khotili motsimikiza kuti: “Palibe chifukwa choti ndichitire manyazi ngati kuti ndapalamula mlandu. Ndikuona kuti chikumbumtima changa pamaso pa Mulungu ndi anthu ndi choyera.”