Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Anastasiya Sycheva

22 JANUARY 2021
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti Mlongo Anastasiya Sycheva Ndi Wolakwa Chifukwa Chochita Misonkhano

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti Mlongo Anastasiya Sycheva Ndi Wolakwa Chifukwa Chochita Misonkhano

Chigamulo

Pa 21 January 2021, khoti la m’boma la Obluchenskiy lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda ku Russia linagamula kuti Mlongo Anastasiya Sycheva ndi wolakwa. Khotili linagamula kuti mlongoyu azikatsatira malamulo ena ali kunyumba kwa zaka ziwiri. Panopa mlongoyu sakufunikira kukakhala kundende.

Zokhudza Mlongoyu

Anastasiya Sycheva

  • Chaka chobadwa: 1977 (Ku Teploozyorsk, M’dera Loima Palokha la Ayuda ku Russia)

  • Mbiri yake: M’banja mwawo anabadwa ana 5 koma awiri anamwalira. Anachita maphunziro a unesi pakoleji inayake ndipo anapeza digiri. Poyamba ankagwira ntchito pachipatala cha mano koma kenako anadzayamba ntchito pachipatala cha anthu a mavuto amaganizo. Mchemwali wake wamkulu atamwalira anavomera udindo wolera ana awiri a mchemwali wakeyo. Ankasamaliranso mayi ake omwe anadwala kwa nthawi yaitali mpaka pamene anamwalira

    Ali mtsikana ankaganizira kwambiri zokhudza mmene moyo wa anthu ulili waufupi. Zimenezi zinachititsa kuti ayambe kuphunzira Baibulo ndipo anapeza mayankho ogwira mtima amafunso omwe anali nawo. Kenako mu 1994, anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova

Mlandu Wake

Mu October 2019, apolisi a ku Russia anaika Mlongo Anastasiya m’gulu la anthu “ochita zinthu zoopsa.” Pa 25 September 2019, dipatimenti yofufuza milandu ya gulu la apolisi achitetezo (FSB) ku Birobidzhan linatsegulira Mlongo Anastasiya mlandu. Mlongoyu akuimbidwa mlandu wochitira dala zinthu ndi gulu la Mboni za Yehova chifukwa choti anapezeka pamisonkhano komanso ankakambirana ndi ena zokhudza chikhulupiriro chake.

Pamene khoti linkamvetsera mlanduwu, oimira boma pamlanduwu anagwiritsa ntchito vidiyo ndi mawu omwe Mlongo Anastasiya ankalankhula pafoni komanso pamisonkhano. Iwo ananena kuti amenewo ndi maumboni osonyeza kuti mlongoyu amachita nawo “zinthu zoopsa.” Komabe, maumboni amenewa anathandiza Mlongo Anastasiya kuti apezerepo mwayi wolalikira. Iye anafotokoza kuti pamisonkhano ya Mboni za Yehova anthu amaphunzira mmene angasonyezere ena chifundo, chisoni, kuleza mtima ndiponso makhalidwe ena ambiri abwino omwe Mkhristu ayenera kukhala nawo.

Mlongo Anastasiya anafotokozanso mmene Baibulo lamuthandizira pa moyo wake pamene ankafotokoza mawu ake omaliza m’khoti. Iye ananena kuti: “Lero ndikuimbidwa mlandu wokhudza chikhulupiriro changa chifukwa chakuti ndikupitiriza kuchita zinthu zokhudza kulambira monga kuwerenga Baibulo, kusonkhana ndi anzanga kuti tikambirane mfundo za m’Malemba, kuimba nyimbo zotamanda Yehova komanso kupemphera.”

Mlongoyu anati: “Kodi ndinganyalanyaze bwanji lamulo lopezeka m’kalata yopita kwa Aheberi m’chaputala 10 mavesi 24 ndi 25, lomwe limati, ‘Ndipo tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.’ Ngati Yehova, Mulungu Wam’mwambamwamba ndi amene amandilimbikitsa kuti ndizisonkhana ndi abale ndi alongo, ndiziwerenga Baibulo, kulimbikitsa ena komanso kuwachitira zinthu zosonyeza kukoma mtima, ndiye ndisamumvere chifukwa chiyani? Ndi Mulungu amene ndimamukonda kwambiri, kumulemekeza ndiponso kumulambira.”

Tikusangalala kwambiri kuona kuti Mlongo Anastasiya anafotokoza molimba mtima zokhudza chikhulupiriro chake komanso anasonyeza kuti ndi wolimba komanso kuti akupitiriza kudalira Yehova. Ndi pemphero lathu kuti Mlongoyu apitirize kukhala wosangalala komanso kuti mayesero amene akukumana nawo alimbitse chikhulupiriro chake ndiponso amuthandize kupitiriza kupirira.