Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 1, 2021
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti Mlongo Tatyana Zagulina Azitsatira Malamulo Ena Ali Kunyumba

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti Mlongo Tatyana Zagulina Azitsatira Malamulo Ena Ali Kunyumba

Pa 31 March 2021, Khoti la m’Boma la Birobidzhan lomwe lili m’dera la Ayuda loima palokha ku Russia linapeza kuti Mlongo Tatyana Zagulina ndi wolakwa. Mlongoyu anauzidwa kuti azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwake kwa zaka ziwiri ndi miyezi 6. Panopa Mlongoyu sakuyenera kupita kundende.