Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 30, 2020
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti a Mboni 4 Ndi Olakwa Ndipo Mmodzi Wamangidwa

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti a Mboni 4 Ndi Olakwa Ndipo Mmodzi Wamangidwa

Pa 30 November 2020, Khoti la m’Boma la Pervomayskiy Mumzinda wa Omsk linagamula kuti M’bale Sergey Polyakov ndi mkazi wake Anastasia komanso Mlongo Gaukhar Bektemirova ndi Mlongo Dinara Dyusekeyeva ndi olakwa.

Khoti linagamula kuti M’bale Polyakov akakhale kundende zaka zitatu ndipo anamutsekera. Pomwe alongo atatuwa anauzidwa kuti azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo kwa zaka kuyambira ziwiri mpaka ziwiri ndi hafu m’malo mokakhala kundende. Ponena mawu ake omaliza m’khoti, M’bale Polyakov ananena motsimikiza kuti: “Yesu ananeneratu kuti chifukwa cha iye, otsatira ake adzawatengera kwa olamulira ndi mafumu kuti ukhale umboni. Malinga ndi zimene Baibulo likunenazi, mlandu wathuwu ndi mbali ya kukwaniritsidwa kwa ulosi wa m’Baibulo n’cholinga choti amene sadziwa za ulamuliro wa Mulungu amve ndi kusankha kukhala kumbali ya ulamuliro wa Mulungu kapena ayi.”—Mateyu 10:18.