FEBRUARY 19, 2019
RUSSIA
Khoti la ku Russia Lagamula Mlandu wa a Dennis Christensen Mopanda Chilungamo Ndipo Lalamula Kuti Akhale M’ndende Zaka 6
Monga mmene chilengezo cha pa 6 February, 2019 chinanenera, khoti la m’boma la Zheleznodorozhniy mumzinda wa Oryol linagamula kuti a Dennis Christensen akhale m’ndende kwa zaka 6 chifukwa cholambira Mulungu mwamtendere. Panopa dongosolo lopanga apilo chigamulochi ku khoti lalikulu lili mkati.
Chigamulo choti a Christensen akhale m’ndende zaka 6 chitangoperekedwa, mabungwe osiyanasiyana analankhulapo. Mabungwe monga Bungwe la Mayiko a ku Europe, Bungwe la European Union, komiti ya ku United States yoona za ufulu wa zipembedzo m’mayiko ena, ofesi ya United Nations ya kazembe woona za ufulu wa anthu, ndi mabungwe ena anena kuti boma la Russia linachita zinthu zopanda chilungamo komanso linalibe chifukwa chomangira a Dennis Christensen.
Kazembe wa nthambi ya United Nations yoona za ufulu wa anthu a Michelle Bachelet, anatulutsa chikalata chomwe mbali yake ina inati: “Chigamulo chankhanza chomwe a Christensen apatsidwa chichititsa kuti a Mboni za Yehova enanso ku Russia azizunzidwa ngakhale kuti ali ndi ufulu wachipembedzo kapena wokhulupirira zimene ukufuna.” Iwo anauza boma la Russia kuti “lisinthe Lamulo Lolimbana ndi Zinthu Zoopsa n’cholinga choti lifotokoze momveka bwino zimene ‘kuchita zinthu zoopsa’ kumatanthauza ndiponso kuti tanthauzolo liphatikizepo kuchita zinthu zachiwawa kapena zoyambitsa chidani.” Pomaliza, a Bachelet anapempha akuluakulu a boma kuti “asiye kuimba milandu komanso atulutse anthu onse amene anawatsekera m’ndende chifukwa chochita zinthu zogwirizana ndi ufulu wawo wopembedza, wofotokoza maganizo awo ndiponso ufulu wosonkhana pamodzi mwamtendere.”
Patangopita masiku awiri chigamulo cha mlandu wa a Christensen chitaperekedwa, akatswiri 4 odziwika bwino pa nkhani za maufulu a anthu ku Russia, anaitanitsa msonkhano wa atolankhani mumzinda wa Moscow. Anthu anadzadza m’chipinda chomwe ankachitiramo msonkhanowu womwe unatenga ola limodzi ndipo anthu ena oposa 6,000 anatsatira pulogalamuyi kudzera pa intaneti. Anthu onse omwe analankhula pamsonkhanowu ananena kuti a Mboni za Yehova ndi anthu amtendere komanso sabweretsa chiopsezo m’dziko.
Enanso omwe analankhula pamsonkhano wa atolankhaniwu anali a Irina omwe ndi mkazi wa m’bale Christensen, a Anton Bogdanov omwe ndi loya wa a Christensen, komanso a Yaroslav Sivulskiy, omwe anaimira bungwe la European Association of Jehovah’s Witnesses. Iwo anafotokoza zokhudza chigamulo chopanda chilungamochi komanso anayankha mafunso omwe atolankhani anawafunsa.
M’bale Christensen akupitirizabe kukhala wosangalala komanso kudalira Yehova ngakhale kuti wakhala ali m’ndende kwa zaka pafupifupi ziwiri. Kutangotsala masiku ochepa kuti chigamulo chiperekedwe, m’bale Christensen anafotokoza maganizo awo komaliza m’khoti kuti: “Pangatalike pangafupike chilungamo cha nkhani chimadziwika, ndipo ndi mmenenso zidzakhalire ndi mlandu wangawu.” Pomaliza, a Christensen atawerenga lemba la Chivumbulutso 21:3-5, ananena motsimikiza kuti: “Mawu amenewa . . . akufotokoza za nthawi pamene Mulungu adzapereka chilungamo komanso ufulu weniweni kwa anthu onse. Ufulu ndi chilungamo zimayendera limodzi. Mulungu adzaonetsetsa kuti zimenezi zakwaniritsidwa.”
M’bale Christensen akhala m’ndende ya Detention Facility No. 1 ku Oryol pamene akuyembekezera chigamulo cha khoti la apilo. Iwo akhala akuwasunga m’ndende imeneyi kwa miyezi 20 yapitayi.
Tipitiriza kupemphera kuti Yehova apitirize kuthandiza a Dennis Christensen, mkazi wawo, komanso a Mboni anzathu onse ku Russia.—1 Petulo 3:12.
Vidiyo yakuti Russian Trial Called ‘A Litmus Test For Religious Freedom’ inapangidwa ndi bungwe lofalitsa nkhani la RFE/RL kutatsala masiku ochepa kuti khoti lipereke chigamulo chake.