Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kumanzere mpaka kumanja: Mlongo Silaeva ndi Mlongo Shamsheva komanso M’bale Khokhlov ndi M’bale Zhinzhikov ali mukhoti pa 28 October 2020

OCTOBER 28, 2020
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lagwirizana ndi Chigamulo cha Khoti Loyamba pa Mlandu wa Abale Awiri ndi Alongo Awiri

Khoti la ku Russia Lagwirizana ndi Chigamulo cha Khoti Loyamba pa Mlandu wa Abale Awiri ndi Alongo Awiri

Pa 28 October 2020, Khoti la m’Chigawo cha Bryansk linagwirizana ndi chigamulo chomwe khoti loyamba linapereka pa mlandu wa M’bale Vladimir Khokhlov ndi M’bale Eduard Zhinzhikov komanso Mlongo Tatyana Shamsheva ndi Mlongo Olga Silaeva. Khoti loyamba linagamula kuti abale ndi alongowa akakhale kundende kuyambira chaka chimodzi mpaka chaka chimodzi ndi miyezi itatu. Komabe, popeza kuti anali atakhala kale m’ndende podikirira kuti milandu yawo izengedwe, sanafunikirenso kukhala m’ndende nthawi ina yowonjezera. Koma chifukwa cha zimene khoti lagamulazi, abale ndi alongowa akhalabe ndi mbiri yoti anapalamula mlandu. Ngakhale kuti zimenezi zawachitikira, iwo akusangalala kuti ndi omasuka. Ndipotu palibenso lamulo lovomereza kuti oimira boma angathe kupanga apilo za nkhaniyi n’cholinga choti abale ndi alongowa akapatsidwe chilango china chokhwima.

Khoti loyamba lisanagamule mlandu wawo, abalewa anakhala m’ndende masiku 316 pomwe alongowa anakhalamo masiku 245 podikira kuti mlandu wawo uzengedwe. Atatulutsidwa m’ndende alongowa anafunsidwa mafunso ndi abale ndipo zomwe anakambirana nawo zinaphatikizidwa mu lipoti la nambala 5 la Bungwe Lolamulira la chaka cha 2020. Iwo anafotokoza kuti kuchita zinthu monga kupemphera, kuwerenga Baibulo komanso kupitiriza kukhala ndi mtima woyamikira kunawathandiza kwambiri kuti apirire mosangalala.