Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 15, 2021
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lakana Apilo ya M’bale Aleksandr Ivshin

Khoti la ku Russia Lakana Apilo ya M’bale Aleksandr Ivshin

Pa 15 April 2021, Khoti la M’Chigawo cha Krasnodar linakana kusintha chigamulo choti M’bale Aleksandr Ivshin akakhale kundende zaka 7 ndi hafu, choncho m’baleyu apitirizabe kukhala m’ndende. Chigamulochi ndi chigamulo chokhwima kwambiri pa zigamulo zonse zimene akhala akupereka kwa Mboni za Yehova, kuchokera pamene boma linaletsa gulu lathu mu 2017.