Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 23, 2020
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lakana Apilo ya M’bale Khasan Kogut

Khoti la ku Russia Lakana Apilo ya M’bale Khasan Kogut

Pa 23 December 2020, Khoti la m’Chigawo cha Kemerovo linakana apilo ya M’bale Khasan Kogut. Izi zikusonyeza kuti chigamulo choyamba chomwe khoti linapereka kuti azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo kwa zaka ziwiri chiyamba kugwira ntchito tsopano. Panopa M’baleyu sakufunikira kupita kundende.

Ngakhale kuti a Kogut ndi okhumudwa chifukwa chakuti kukhala ndi mbiri yopalamula mlandu kuipitsa dzina lawo monga nzika ya dziko la Russia, iwo sakudandaula podziwa kuti sanasiye kukhala okhulupirika komanso akusangalatsa mtima wa Yehova. A Kogut limodzi ndi akazi awo a Yekaterina komanso mwana wawo Timofey wazaka 8, onse ndi otsimikiza mtima kuti apitiriza kutumikira Yehova monga banja.

M’mawu awo omaliza omwe ananena m’khoti pa 10 September 2020, a Kogut ananena molimba mtima kuti: “Sindingasiye kukhala wokhulupirika kwa Yehova Mulungu ndipo ndikuona kuti ndi mlandu kundikakamiza kuti ndisiye Yehova. Sindingasiye kutsatira zimene ndimakhulupirira. Ndipo kaya ndikumane ndi zotani, zinthu monga ‘imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, mphamvu, msinkhu, kuzama, kapena cholengedwa china chilichonse, sichidzatha kundilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu.’”—Aroma 8:38, 39.