Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JANUARY 19, 2021
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lakana Apilo ya M’bale Sergey Ledenyov

Khoti la ku Russia Lakana Apilo ya M’bale Sergey Ledenyov

Pa 19 January 2021, Khoti la m’Chigawo cha Kamchatka linakana apilo ya M’bale Sergey Ledenyov. Izi zikusonyeza kuti chigamulo chimene khoti linapereka poyamba choti azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwa zaka ziwiri chiyamba kugwira ntchito tsopano. Panopa sakufunika kukakhala kundende.

Khoti lisanapereke chigamulo chake, a Ledenyov analankhula pamaso pa khoti. Iwo analankhula molimba mtima za chikhulupiriro chawo ndipo ananena motsimikiza kuti sasiya kulambira Yehova. Iwo anati: “Zimene ndimakhulupirira sikuti zangokhala malamulo amene gulu linalake linakhazikitsa koma ndi zochokera m’Baibulo. Mwachitsanzo, ndimakhulupirira kuti ‘nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu’ komanso kuti ‘Dzina lake ndi Yehova.’ (Aheberi 3:4; Ekisodo 15:3)

Palibe chigamulo cha khoti chimene chingafufute mawu amenewa m’Baibulo kapena mumtima mwanga.”