Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

16 JUNE 2021
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lakana Apilo ya M’bale Sergey Verkhoturov

Khoti la ku Russia Lakana Apilo ya M’bale Sergey Verkhoturov

Pa 16 June 2021, khoti la m’Chigawo cha Nizhny Novgorod linakana apilo ya M’bale Sergey Verkhoturov. Zimenezi zikutanthauza kuti chigamulo chimene khoti linapereka poyamba choti m’baleyu azitsatira malamulo ena ali kunyumba, sichinasinthe. Panopa sakufunikira kupita kundende.