Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 22, 2021
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lakana Apilo ya Mlongo Reyno-Chernyshova

Khoti la ku Russia Lakana Apilo ya Mlongo Reyno-Chernyshova

Pa 22 April 2021, khoti lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda linakana apilo ya Mlongo Yelena Reyno-Chernyshova. M’malomwake, khotili linavomera apilo ya loya woyimira boma pa milandu kuti mlongoyu amusinthire chigamulo chimene anamupatsa poyamba choti apereke chindapusa cha ndalama zokwana madola 135 a ku America n’kum’patsa chilango chokhwima choti azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwake kwa zaka ziwiri ndi miyezi 6. Panopa mlongoyu sakuyenera kupita kundende.