NOVEMBER 17, 2020
RUSSIA
Khoti la ku Russia Lakana Apilo ya a Mboni Atatu
Pa 17 November 2020, Khoti la M’chigawo cha Kamchatka linakana apilo yokhudza mlandu wa M’bale Konstantin Bazhenov, mkazi wake Snezhana ndi Mlongo Vera Zolotova. Zimenezi zachititsa kuti chigamulo chimene khoti linapereka poyamba choti azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo kwa zaka ziwiri chiyambe kugwira ntchito tsopano. Panopa sakuyenera kupita kundende. Ngakhale kuti akumana ndi zimenezi, iwo adakali okhulupirika ndipo akusangalalabe.
Pa nthawi imene khoti linkamalizitsa kuzenga mlandu pa 25 September 2020, M’bale Bazhenov anauza woweruza molimba mtima kuti sakuopa kuzengedwa mlandu. Iye ananenanso kuti akuona kuti ndi mwayi kuti mawu a Yesu a pa Yohane 15:20, akukwaniritsidwa pa iyeyo. Palembali Yesu ananeneratu kuti otsatira ake adzazunzidwa.
M’bale Bazhenov anafotokozanso kuti pa Mateyu 28:19, 20, Yesu analamula ophunzira ake kuti azilalikira. Kenako M’bale Bazhenov anafunsa molimba mtima kuti: “Ndani amene ali ndi ufulu wothetsa kapena kuletsa lamulo limene Khristu anapereka?” Ndiye ananena kuti: “Sindingathe kukhala chete. . . . Ndipitiriza kuuza anthu uthenga wabwino wochokera m’Baibulo.”