Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

28 JULY, 2020
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lalamula kuti M’bale Yevgeniy Spirin Apereke Ndalama Zoposa Madola $6,900

Khoti la ku Russia Lalamula kuti M’bale Yevgeniy Spirin Apereke Ndalama Zoposa Madola $6,900

Pa 28 July 2020, khoti la mumzinda wa Furmanovsky, m’chigawo cha Ivanovo linagamula kuti M’bale Yevgeniy Spirin ndi wolakwa. Oweruza ananena kuti m’baleyu ayenera kukhala kundende zaka 7. Koma kenako khoti linanena kuti m’malomwake alipire chindapusa cha marubo 500,000 (Madola 6,920 a ku United States). M’bale Spirin adzachita apilo.