Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Anatoliy Tokarev ali panja pa khoti mu August 2020

OCTOBER 23, 2020
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lalipiritsa Chindapusa M’bale Anatoliy Tokarev

Khoti la ku Russia Lalipiritsa Chindapusa M’bale Anatoliy Tokarev

Pa 23 October 2020, Khoti la m’Boma la Oktyabrsky m’Chigawo cha Kirov linapeza kuti M’bale Anatoliy Tokarev ndi wolakwa ndipo linagamula kuti alipire chindapusa cha ndalama zokwana madola 6,552 a ku United States. A Tokarev ali ndi masiku 10 oti achite apilo chigamulochi.

M’mawu ake omaliza m’khoti, M’bale Tokarev analankhula molimba mtima kuti: “Mmene ndikuonera, apolisi akundiuza mosabisa mawu kuti: ‘Kuli bwino usankhe kuti wasiya zomwe umakhulupirira, apo ayi . . . udzazunzidwa moipa.’ . . . Olemekezeka, zomwe ndilankhule panozi ndinazilankhulaponso pa tsiku loyamba la mlanduwu. Ndipo ndikubwerezanso panopa kuti, sindingasiye kutsatira zomwe ndimakhulupirira ponena za Mulungu. . . . N’zoona kuti ndimachita mantha apolisi akamandiopseza kuti andimanga kapenanso kuti andipha ndipo umu ndi mmene wa Mboni za Yehova aliyense angamvere. Komanso apolisi akamanena kuti ndimachita zinthu zoopsa amakhala akundiwonongera mbiri ngakhale kuti sindinalakwe chilichonse. Ndiponso china choti mudziwe Olemekezeka, ndi chakuti sindingakane Mulungu ndipo sindingalole kuti asiye kundikonda.”