Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Aleksey Metsger, akuganiziridwa kuti ndi wolakwa ndipo khoti la ku Russia lamulipiritsa chindapusa chifukwa cha chikhulupiriro chake

NOVEMBER 21, 2019
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lalipiritsa M’bale Aleksey Metsger Chindapusa cha $5,460 Koma Lakana Zoti Akhale M’ndende

Khoti la ku Russia Lalipiritsa M’bale Aleksey Metsger Chindapusa cha $5,460 Koma Lakana Zoti Akhale M’ndende

Lachinayi pa 14 November, 2019, khoti la m’boma la Ordzhonikidzevskiy mumzinda wa Perm, linagamula kuti M’bale Aleksey Metsger ndi wolakwa ndipo linamulipiritsa chindapusa cha ndalama pafupifupi madola 5,460 a ku America. M’baleyu ndi wa nambala 12 pa abale omwe chaka chino akuganiziridwa kuti anapalamula mlandu wochita zinthu zoopsa ku Russia, ngakhale kuti sanalakwe chilichonse ndipo ankangolambira Mulungu mwamtendere ndiponso ankauza ena za Mulungu. Loya wa M’bale Metsger akapanga apilo chigamulochi.

M’bale Metsger anayamba kuimbidwa mlandu pa 25 April, 2019, chifukwa choti ankanena kuti ndi wa Mboni za Yehova. Anthu omwe M’bale Metsger ankakambirana nawo zokhudza chipembedzo ankajambula mobisa zomwe ankakambiranazo ndipo ndi zina mwa zinthu zimene zinagwiritsidwa ntchito ngati umboni pa mlanduwu.

Khoti linayamba kuzenga mlanduwu pa 14 October, 2019. Loya woimira boma mumzinda wa Perm anapempha kuti M’bale Metsger apatsidwe chilango choti akakhale m’ndende kwa zaka zitatu. Ngakhale kuti khoti silinagamule kuti m’baleyu akhale m’ndende, linanena kuti ndi wolakwa ndipo anapatsidwa chilango. Choncho ndife okhudzidwa chifukwa zimenezi zikhoza kuchititsa kuti makhoti ena ayambe kuimba milandu abale ndi alongo athu enanso ambiri.

Pamene akuluakulu a boma akupitiriza kuzunza abale athu ku Russia popanda zifukwa zomveka, tikudziwa kuti Yehova apitiriza kuwatonthoza komanso kuwalimbikitsa.—Salimo 119:76, 161.