Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

14 FEBRUARY, 2020
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lalipiritsa M’bale ndi Mlongo Popov

Khoti la ku Russia Lalipiritsa M’bale ndi Mlongo Popov

Pa 14 February, 2020, khoti la mumzinda wa Vilyuchinsk linaweruza mlandu wa M’bale Mikhail Popov ndi mkazi wake Yelena Popova. Khotilo linalamula kuti M’bale Popov apereke ndalama zokwana marubo 350,000 (Madola 5,508 a ku United States) ndipo mlongoyu apereke marubo 300,000 (Madola 4,722 a ku United States) koma silinagamule kuti akakhale kundende. M’bale ndi mlongoyu akufuna kuchita apilo.

Mikhail ndi Yelena anamangidwa mu July 2018 koma pasanapite nthawi yaitali anamasulidwa poyembekezera mlandu wawo.

Kuyambira mu 2019, makhoti a ku Russia akhala akuzenga milandu ya a Mboni za Yehova 28 yokhudza chikhulupiriro chawo. Pa anthu amenewa, abale ndi alongo 10 azengedwa mlandu miyezi iwiri yapitayi koma sanatsekeredwe m’ndende.